Nkhani

Escom, ganizirani Amalawi

Listen to this article

Utsi sufuka popanda moto. Mwambiwu umatanthauza kuti kalikonse kamveka sikatero pachabe.

Zamveka kuti bungwe la Escom likufuna kukweza magetsi, tikukhulupirira kuti izi sizidangolankhulidwa, kenakake bungweri likukonza.

Escom idziwe kuti Amalawi amafuna zinthu zotsika mtengo komanso zoyenerera. Nthawi zonse pamene akukweza magetsi amanena kuti akufuna kukonza zinthu kuti magetsi asamazimezime yomwe imangokhala nyimbo.

Tikulankhulamu magetsi akungozimazima pena mpaka kumatha tsiku lonse magetsi osayaka. Pamene azimitsa magetsi kodi amaganiza kuti anthu akugwiritsira ntchito chiyani? Makalanso ndi oletsedwa ndiye anthu agwire mtengo uti?

Bungwe la Escom liganize lisadabwere ndi chiganizo. Tikukamba kuti kuchokera mu May chaka chatha akweza magetsi katatu. Ngakhale adakweza Amalawi sadaone kusintha kulikonse chifukwa kuzimba kwa magetsi ndiyo yakhala nyimbo yomwe aliyense akuyimba.

Chonsecho tikumva kuti kampaniyi yagula galimoto zodula zedi masiku apitawa.

Amalawi akufuna magetsi tsiku lonse komanso nthawi zonse. Magetsi akenso akhale otsika mtengo osati akwere ngati akakwera asintha kanthu. Zinthu zidakwera inde koma m’Malawi aliyense akulira si inu nokha a Escom amene mukumva kuwawaku.

Kondani Amalawi osati kukweza zinthu.

Related Articles

One Comment

  1. Kodi ESCOM ili ndi maganizo owonjezera ma galimoto ena? Chifukwa nchachiziwikire kuti sangathese vuto lakuzimazima kwamagetsi. Iwo cholinga chawo nkubera a Malawi omwe pakadali pano akuvutika kugwira ntchito usiku ndi usana kuti apeze ndalama.

Back to top button