Nkhani

Amayi tizivulana tokhatokha?

Listen to this article

Pali zinthu zina zoti mnzako akachita owonawe umazizwa, kuchita kakasi kuti kodi winayo waganiza bwanji?

Mwachitsanzo, pali zakudya zina zoti kumuona wina akutafuna, iwe umasowa mtendere. Chimodzimodzi mavalidwe; pali zovala zina zimadabwitsa kuti kodi mayiyu kapena bamboyu analimba mtima bwanji kutuluka m’nyumba mwake akuoneka tere.

Nkutheka ichi nchifukwa chake amayi ena ku Lilongwe adadabwapo masiku apitawa ndi mmene mayi mnzawo adatulukira m’nyumba mwake atavala mini.

Koma mmalo mongolekera podabwapo, amayiwa adatengera zinthu pamgong’o nkumuvula mnzawoyo kuti akhale mbulanda ati nzomwe amafuna.

Kodi anzanga, mmene tachulukira m’dziko muno, munthu nkumayembekeza kuti onse achite zofuna zako ndithu?

Anthufe takulira kosiyana zomwe zimachititsa kuti kavalidwe kathu, kakonzedwe ka tsitsi ndi zokonda zina zilekane.

Kuonjezera apo, ntchito kapena bizinezi zomwe tikuchita nzosiyana zomwe zimachititsanso kuti maonekedwe athu asiyanenso.

Nthawi ndi nthawi tonsefe timaona ndithu zosatikondweretsa pa matupi a ena. Tsitsi lina ukaliwona umalakalaka utalimeta; magalasi ena wina akavala ngati ukamutaire; wina akakhwefula thalauza ngati ukamukwezere.

Koma izi sizingathandize chifukwa ubwino ndi kuipa timakudziwa mosiyana Pamene wina amakonda kuti miyendo yake ikhale poonekera, wina amati ine yangayi ndiyibise.

Wina akukonda zothina, wina amati koma zotaya. Pamene mnyamata wina akonda chiuno cha thalauza yake chikhale mchimake, wina amati chake chikhale mmusi.

Pozindikira kulekana kwa zofuna za anthu, padakhazikitsidwa ufulu wa kavalidwe kuti aliyense avale umo zingamukomere. Ubwino wake aliyense ali ndi lake thupi lake.

Ndipo malinga ndi malamulo, mphamvu zomwe munthu angakhale nazo pakavalidwe zimathera pathupi lake osati lawina.

Tsono khalidwe lofuna kuti anthu achite zofuna zathu kapena molingana ndi mmene ife tifunira ndilosathandiza komanso lolakwira lamulo.

Izi mwina ukhoza kuchita ndi mwana kapena mbale wako, koma osati munthu wadera ongokumana naye pamsewu. Zilibe kanthu kuti walaula bwanji winayo, mleke. Samala za thupi lako chifukwa ulibiretu mphamvu yokakamiza wina kuti avale mwakufuna kwako.

Related Articles

Back to top button