Nkhani

Flames ikaluza, Tom abwerera?

Listen to this article

Kuli nkhondo ku Calabar lero. Flames ikhala ikuphana ndi Nigeria masewero amenenso aunikire ntchito ya mphunzitsi wa Flames Tom Saintfiet.

Kupambana kwa lero kuthandiza Uncle Tom kuti mwina apate ntchito yophunzitsa Flames.

Aganyu lero tili pambuyo pa Flames monga tichitira ngakhale kupambana kwalero kufunika Mulungu akhale mbali yathu.

Pemphero lathu tigwirana manja ndi mneneri wa ku Chirimba mumzinda wa Blantyre yemwe wabwera poyera kuti waona Flames ‘ikupita pagolo la Nigeria kawiri.’

Ulosiwu mwina ukutanthauza kuwina chifukwa mawu a mtumikiyu akuti ‘kupita pagolo,’ ndiye sitikudziwa ngati kupita pagolo kuli kuchinya kapena kungopitapo.

Tafuna timvetsetsane apa chifukwa mneneri winanso ku Zomba adalosera kuti akuona Amalawi titanyamula mbendera yathu uko tikusangalala. Iye amalankhula pamene Flames imakumana ndi Namibia. Pamapeto pake tidalepherana mphamvu. Ndiye pena tikuyenera kumvetsa zomwe oloserawa akunena.

Koma nkhani ilipo ndi ya Uncle Tom. Kodi tikagonja lero abwereranso kumudzi kuno? Kudzatani? Tikufunsa choncho chifukwa iwo adati loto lawo ndi kugwetsa Nigeria basi, ngati Nigeria siigwa ndiye abweranso? Kapena atengeratu katundu wawo?

Ife ndi okonzeka kukhala ndi Uncle Tom bola zomwe anabwerera zitheke. Tonse tili pambuyo pa Flames kuti iwine lero.

Pamene maso akhale ku Calabar, aganyu tikhale tili ku Mzuzu kumene Moyale ikhale ikuphana ndi Red Lions mu mchikho cha Carlsberg komanso mawa tikumana pa Kamuzu pamene jombo ya Kamuzu Barracks ipondane ndi mphembedzu za Blantyre United.

Related Articles

Back to top button