Fisp yabwerera m’bwalo
Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika Lachisanu adalengeza kuti ndondomeko ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo yabwerera ku Farm Input Subsidy Programme (Fisp) kuchoka ku Affordable Inputs Programme (AIP).
Cholinga cha ndondomeko ziwirizi n’chimodzi koma zimangosiyana kachitidwe kake, monga kasankhidwe ka alimi oyenera kupindula pomwe Fisp imadalira mafumu ndi makomiti achitukuko, opindula mu AIP amasankhidwa m’maere.

Mneneri wa unduna wa za ulimi a Arnold Namanja atsimikiza kuti ntchito yosankha opindula idali mkati m’midzi m’sabata ikuthayi ndipo maina akuyembekezeka kupita kulikulu la za malimidwe.
“Mafumu ndi makomiti ndiwo akusankha anthu opindula ndipo izi zimachitikira poyera aliyense akuona. Alangizi a za malimidwe ndiwo amachitira umboni posankhapo kuti pasakhale chinyengo,” atero a Namanja.
Iwo ati likulu la za malimidwe limapereka mlingo wa alimi oyenera kupindula pa khonsolo iliyonse ndipo pakhonsolopo, amaona kuti agawa bwanji m’madera a mafumu onse.
“Khonsolo ikapatsidwa nambala, akuluakulu amakhala pansi n’kuona kuti agawa bwanji kutengera kukula kwa midzi ndi chiwerengero cha omwe akukwanira pa zolinga za pulogalamu,” adatero a Namanja.
Fisp idayamba m’bajeti ya 2005/06 ndipo cholinga chake n’kupindulira alimi ang’onoang’ono omwe ali ndi malo olimapo komanso ali ndi mphamvu zolimira. Kwenikweni, pulogalamuyi imalonda maanja ovutikitsitsa makamaka oyendetsedwa ndi nkhalamba, amayi, ana amasiye ndi aulumali.
Tonse Alliance italowa m’boma, idasintha Fisp n’kuyambitsa AIP pomwe likulu la za ulimi limagwiritsa ntchito kaundula wa alimi posankha opindula ndipo amadziwa podzera pa lamya za m’manja ndi cholinga chofuna kuchepetsa kukondera komwe alimi ankadandaula kuti kumachitika mayina akamasankhidwa ndi mafumu.
Alimi ena auza Tamvani kuti kubwezeretsa mphamvu kwa mafumu ndi makomiti kukhoza kubweretsanso mavuto okondera omwe adalipo kale zomwe zingachititse kuti pulogalamuyo isakhale yaphindu.
“Cholinga cha pulogalamuyi n’chabwino koma kuibwezeretsa kwa mafumu kukhoza kusokoneza cholingacho. Zidali bwino pomwe mayina ankasankhidwa ndi anthu oti sakudziwa aliyense chifukwa pamudzi zimalowa kuyang’ana nkhope yamunthu,” adatero a Danniel Mtambo wochokera kwa Dzoole ku Dowa.
Nawo a Lyton Alfred wochokera kwa Chitukula ku Lilongwe ati mafumu amatengerapo danga nkumayika mayina a abale awo ndi anthu ena oti sakuyenera kupezeka pamndandanda opindula kusiya ovutika enieni.
Koma amfumu a Kalonga aku Salima ati boma lachita bwino kubwezeletsa Fisp ndi mphamvu kwa mafumu ndi makomiti chifukwa ndiwo amadziwa anthu enieni oyenera kupindula.
“Zimawawadi kwa omwe s ada s an k h i d we koma dziwani kuti tili mu nthawi ya kusavomereza, zimaoneka ngati pachitika kokera kwako kwa omwe sadasankhidwe koma chilungamo nchoti pamudzi m’madziwana bwino nokhanokha,” atero a Kalonga.
Iwo adagwirizana ndi dandaulo la mafumu ena kuti amapatsidwa mayina ochepa pomwe ali ndi maanja ovutika ambiri ndiye zimavuta kuti asankhe ndani ndipo aside ndani ndipo osiyidwawo amawona ngati padali kukondera.
Mdziko muno muli alimi ang’onoang’ono pafupifupi 3.1 miliyoni koma mundondomeko yachaka chino yomwe itsegulidwe mkati mwa mwezi uno, alimi 1.1 miliyoni akuyembekezeka kupindula kutanthauza kuti alimi 2 ang’onoang’ono miliyoni ayima pawokha.
Kadaulo pazaulimi a Leonard Chimwaza adati pulogalamuyi itayendetsedwa bwino ikhoza kusintha kapezekedwe kachakudya mdziko muno.
Kadaulo wina a Tamani Nkhono Mvula adati alimi asamadikile kuti mayina azipangizo zotsika mtengo atuluke kuti aziyamba kusaka kolowera koma aziyambiratu kupanga manyowa akangokolola kuti f e tereza az ikha la ongowonjezera.



