Gule wamkulu akusokoneza
Atsogoleri omwe anali ku msonkhano wa Unesco wokhudza kuteteza masewera a chikhalidwe adaonetsa kuda nkhawa ndi kukula kwa chiwerengero cha ana amene akusiya sukulu ndi kukalowa gule wamkulu.
Polankhula pa msonkhanowo ku Thope Lodge ku Mponela m’boma la Dowa Lachitatu, mkulu wa maphunziro Mayi Alexina Gompho-Mtingwi ati khalidweli lafala kwambiri ndipo likukhudza kapitidwe ka ana ku sukulu.

“Masiku ano mumapeza ana a zaka 15 kapena ocheperapo akusuta fodya ndi kuvala ngati Gule Wamkulu mmalo mopita ku sukulu. Izi zikuchitika m’matauni ndi m’ma trading centre, osati m’midzi yokha,” adatero iwo.
Mfumu Yaikulu Yobe Njolomo Mpatang’ombe ya ku Ntchisi idapempha chilango chokhwima pokhudzana ndi ana amene akuchita khalidweli.
“Ana aang’ono amenewa ayenera kusamalidwa mosamala. Muli ndi ufulu kuwagwira ndi kuwapereka ku apolisi kuti alandire malangizo,” adatero iwo.
Iwo adaonjezera kuti ambiri mwa ana omwe akutsanzira Gule Wamkulu si a Chichewa ndipo zochita zawo zikuononga chikhalidwechi.
“Pochita izi akunyazitsa Gule Wamkulu. Ambiri mwa iwo sikuti ndi Achewa, ndipo izi zikuononga chikhalidwe chathu. Ayenera kulangizidwa asanasokere,” adatero iwo.
Nkhawazi adazitula pa zokambirana za Unesco za pulojekiti ya Safeguarding Ludodiversity yomwe ikufuna kuphatikiza masewera achikhalidwe ndi miyambo m’maphunziro.
Nthumwi zidagwirizana kuti ngakhale Gule Wamkulu ndi gawo lofunika kwambiri la chikhalidwe cha Malawi, kugwiritsira ntchito molakwika ndi ana a sukulu kukuopseza maphunziro awo komanso ulemu wa mwambowo.
Msonkhanowo udasonkhanitsa atsogoleri a chikhalidwe, akuluakulu a maphunziro komanso oimira masewera ndi maphunziro a m’bomalo.


