Nkhani

Mabwana a apolisi akana kusamuTsidwa

Bwalo lalikulu la milandu ku Lilongwe laletsa boma kusamutsa akuluakulu a apolisi asanu omwe analamulidwa kuti achoke ku polisiko ndi kupita ku maunduna a boma ndi malo ena.

Apolisi asanuwa, omwe anali pa maudindo a ukomishonala, ndi a Christopher Katani, a Rhoda Manjolo, a Emmanuel Soko, a Chikondi Chingadza ndi a Barbara Mchenga Tsiga.

Nawonso akuti asamutsidwe: A Chingadza. | Nation

“Tikulamula kuti boma kapena aliyense oyimira boma kuti asasamutse apolisi amenewa kupita kuli konse mpaka khotili lilamule kapena mulandu wawo uthe,” uthenga wa khoti watero mu chigamulo chake cha pa Novembara 28 2025.

Woweruza milandu William Yakuwawa Msiska anaperekanso mwayi kwa apolisiwa kuti atha kukapereka madandaulo awo ku khoti.

Mkulu wa za malamulo m’dziko muno a Frank Mbeta anati sadachione chigamulocho choncho chikhala chovuta kuti alankhulepo.

Mlembi wamkulu ku ofesi ya mtsogoleri wa dziko lino ndi nduna a Justin Saidi anati apatsidwe nthawi kuti ayankhepo pa nkhaniyo kaamba koti ayenera kulankhula kaye ndi mkulu wa za malamulo m’dziko muno.

A Katani anali mkulu wa polisi ku chigawo cha kumpoto, a Tsiga chigawo chapakati ndi kuvuma, a Chingadza chigawo cha kuzambwe, a Soko chigawo cha kum’mwera ndi kuzambwe ndipo a Manjolo anali wa chigawo chapakati ndi ku kuvuma.

Sabata yatha, woweruza milandu ku bwalo laikulu a Kenyatta Nyirenda anawonso adapereka chiletso choti boma lisasamutse akuluakulu a asilikari kukagwira ntchito kwina.

Asilikariwa ndi a Chikunkha Soko, a Saiford Kalisha, a Swithan Mchungula, a Kakhuta Banda ndi a Harold Dzoole.

Iwo anatumidzidwa ku Electricity Supply Corporation of Malawi, National Oil Company of Malawi, Agricultural Development and Marketing Corporation ndi ku Electricity Generation Company.

Mneneri wa makhoti a Ruth Mputeni anati cholinga cha chiletsocho nkuletsa boma kutumiza akuluakuluwa asalamulidwe kukagwira ntchito kwina mpaka nkhani yawo itawunikidwa bwino. 

Pokambapo pa nkhani ya sabata yatha, katwiri pa za chitetezo a Master Dicks Mfune anati zomwe boma linachita kunali kudutsa malire chifukwa lilibe mphamvu zimenezo koma khonsolo ya asilikari (MDF Council).

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Check Also
Close
Back to top button