Nkhani

HRDC ikufunabe zionetsero m’zipata

Gulu lomwe likutsogolera zionetsero zofuna kuchotsa wapampando wa bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) Jane Ansah la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) laimitsa zionetsero kuti lipeze njira yochotsera chiletso chotseka mabwalo a ndenge ndi zipata za dziko lino.

Bungwe loona za misonkho la Malawi Revenue Authority (MRA) adakamang’ala kuti zionetsero zisachitike kumalowo chifukwa zisokoneza ndalama zimene limatolera.

Bungwelo lidaimitsa zionetsero zomwe zimayenera kufika dzulo zionetserozo zitangochitika Lachitatu lokha pomwe zidakoka makamu a anthu m’maboma a Karonga, Mzuzu, Zomba, Lilongwe ndi Blantyre.

Wachiwiri kwa wapampando wa bugwelo Gift Trapence Lachinayi adati zionetsero sizipitirira Lachinayi ndi Lachisanu ngati momwe chikonzekero chidalili kuti akuluakulu a bungwelo akumane ndi

owayimilira pa mlandu.

“Taimitsa zionetsero pofuna kupeza njira yochotsera chiletso chokatseka m’mabwalo a ndenge ndi zipata zotulukira m’dziko lino. Khumbo ilili tikadali nalo chifukwa mwina ndi njira yokhayo yomwe angamvere pempho lathu,” adatero Trapence.

Koma ngakhale HRDC idati zionetserozo ziime, anthu ena ku Mzuzu Lachinayi adapitabe pamsewu kukachita zionetsero zofuna kuti Ansah atule pansi udindo.

Katswiri pa ndale George Phiri adati akugwirizana ndi zomwe HRDC yapanga poimitsa zionetserozo kuti ligundane mitu mozama ndi

owaimira pamilandu kuti apeze njira yomwe ingatsegule pakamwa pa akuluakulu a boma.

“Anthu akapereka kalata ya madandaulo, amayembekezera kuti ayankhidwa ndi ofesi yomwe ayilembera kalatayo, ndiye ngati akungopereka kalata koma osayankhidwa, ndiye kuti pena pake pali vuto. Tsono alekeni afufuze pali vutopo,” adatero Phiri.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button