Kamangila wakwekwesa jaji
Woweruza milandu ku khoti la za chuma a Kenan Manda ati mmodzi mwa maloya odziwika a Alexious Kamangila awapepese kaamba ka zomwe adalemba patsamba lawo la mchezo zokhudza Jajiyo.
A Kamangila adalemba pa tsamba la mchezo nkhani zomwe ena akutanthauzira kuti a Manda satha ntchito yawo yoweruza komanso ndi a katangale.

Malingana ndi a Manda, zomwe adalemba a Kamangira z i d a w a o n o n g e r a m b i r i yawo kotero akufuna kuti a Kamangirawo alembenso patsamba lomwelo sawapepesa a Manda.
Loya wa a Manda a Michael Goba Chipeta adatsimikiza kuti adasumira a Kamangila pa nkhaniyo ndipo mlandu uli ku khoti komanso kuti khoti lidapereka chiletso choti a Kamangila asapitirize kulemba zonyazitsa a Manda.

“Tidawatumizira kale kalata ya chiletsocho komanso a ku khoti adawaimbira lamya kuwauza kuti kalata zina zili ku khoti. Apapa ndiye kuti sakuyeneranso kulemba chilichonse chokhudza a Manda,” adatero a Chipeta.
Kupatula chipepeso chomwe a Ma n d a a ku f u n a , iwo atinso akufuna a Kamangila awapatse ndalama zokwana K250 mi l i y oni chi fukwa chowaipitsira dzina ndi kuwachotsa ulemu.
Magulu osiyanasiyana k u p h a t i k i z a p o mabungwe omwe si aboma aikira ndemanga z a w o m a k a m a k a zounikira kuti a Manda afufuzidwe pa nkhani zomwe a Kamangira a d a u l u t s a z o k u t i chilungamo chidzaoneke.
Bungwe la achinyamata la Youth and Society (YAS) lati chilungamo c h o m w e A m a l a w i angapindule pa nkhaniyo ndi kafukufuku komanso ochita kafukufukuyo akuyenera kudzalengeza zomwe adzapeze.
M’kalata yake yomwe idatuluka mkati mwa sabatayi, bungwe la YAS lidati maso ake ali pa nkhaniyo kuti mpakana lidzaone mapeto ake ndi chilungamo chake.
Mkati mwa sabata yomweyo, a Kamangira adaopseza kuti ali ndi umboni onse wokhudza nkhani zoti a Manda adachita za katangale poweruza nkhani zina ku bwalo lawo la milandu.
Izi zili choncho, maloya anzawo a a Kamangila adawaikira kumbuyo n’kuwalimbikitsa kuti asafooke pa nkhaniyo ndipo ku t i m a l o y a enawo ndi wokonzeka kuwathandizira kuti chilungamo chidziwike.
Padakalipano komiti ya ku Nyumba ya Malamulo yati iitanitsa a Manda kuti akayankhe nkhani zaphulikazo. Atawapeza olakwa, aphunguwo a l i n d i m p h a m v u zowachotsa pa mpando wawo.



