Nkhani

Kalembera wa chisankho ayamba lolemba lomweli

Kalembera wa chisankho cha 2025 ayamba Lolemba likudzali pomwe zipani zakangalika kumema anthu ozitsatira kuti akalembetse mwa unyinji kuti adzakhale ndi mpata wokavota.

Kupatula zipani za ndale, bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lati ndi lokonzeka kulemba anthu onse oyenera kulembedwa m’kaundulayo.

Anthu kulembetsa m’kaundula mmbuyomu

Wapampando wa MEC mayi Annabel Mtalimanja atsindika kuti makina ochitira kalemberayo adayesedwa ndipo alibe vuto lililonse komanso anthu odzachita kalemberayo adaphunzitsidwa mokwanira kagwiritsidwe ntchito ka makinawo.

“Zonse zili bwino, makina akugwira bwino ntchito komanso maphunziro a ochita kalemberayo adachitika moti adauzidwa kale komwe adzagwirire ntchito ndi zoyenera kudzatsata kumeneko,” adatero a Mtalimanja.

Nalo bungwe lophunzitsa anthu la National Initiative for Civic Education (NICE) Public Trust lati ntchito yophunzitsa anthu za kalembera komanso kaponyedwe Ka voti idayenda bwino.

Mneneri wabungwelo mayi Grace Hara ati bungwelo lidazungulira m’madera monse kufikira anthu ndi maphunziro okhudza zisankho moti pali chikhulupiliro choti ambiri akudziwa zambiri zokhudza chisankho.

“Ife ntchito tagwira moti apapa tikhoza kunena molimba mtima kuti anthu akudziwa zochita. Komabe sitikulekera pomwepo chifukwa pali zambiri zofunika anthu atauzidwa moti tikadali kalikiliki,” adatero a Hara.

Kadaulo pa ndale a Ernest Thindwa ati Amalawi ambiri akuonetsa chidwi chodzaponya voti kotero akuyembekeza kuti kuyambira Lolembali, anthu akhamukira kokalembetsa m’kaundula.

“Anthu akuonetsa kuti akuzindikira kufunika kwa voti yawo, ichi n’chomwe chikupeleka chiyembekezo kuti anthu ambiri akalembetsa. Komanso kulembetsa kokha n’kosakwanira koma adzaponya voti mwa unyinji,” adatero a Thindwa.

Iwo ati khumbo la anthu lodzaponya voti likhoza kukhala lopanda tanthauzo ngati anthuwo sangapatsidwe mpata makamaka pochotsa zonse zokhomerera.

Iwo adanena ndemangayi potsatira kulira kwa andale ena makamaka otsutsa boma omwe sakugwirizana ndi ganizo lodzagwiritsa ntchito zitupa za unzika ponena kuti ena alibe zitupazo.

Mneneri wachipani chotsutsa cha Democratic Progressive (DPP) a Shadric Namalomba adati chipani chawo sichikugwirizana ndi ganizo logwiritsa ntchito zitupa za unzika.

“Dandaulo lathu ndi loti anthu ambiri sadalembetse za unzika koma ndi anthu oyenera kudzaponya voti. Anthu ngati amenewa tikuona kuti ufulu wawo udzaphwanyidwa chifukwa sadzatha kulembetsa m’kaundula,” adatero a Namalomba.

Koma a Mtalimanja adati anthu asade nkhawa ndi za unzika chifukwa bungwelo lapanga kale dongosolo loti pa malo ali onse olembetsera pazidzakhalanso a kalembera wa unzika.

“Palibe chodetsa nkhawa ayi chifukwa munthu aliyense oyenera kuvota adzapatsidwa mpata. Polembetsera paliponse pazidzakhala a NRB kuti omwe alibe za unzika azidzayamba kulembetsa cha unzika kenako n’kupita polembetsera zisankho,” adatero a Mtalimanja.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button