Nkhani

Kauniuni wa AIP watentha

Listen to this article

Makomiti a Nyumba ya Malamulo omwe akuunika momwe feteleza wa AIP adagulidwira kuti ndalama zina zokwana K750 miliyoni zisokonekere aluma mano kuti akufuna aone 1 tambala yomalizira itabwezedwa.

Makomitiwo anena izi kampani ya boma yoona za feteleza ya Smallholder Farmers Fertilizer Revolving Fund of Malawi (SFFRFM) itauza makomitiwo kuti mwa K750 miliyoni, K187 miliyoni yabwezedwa kale.

Ganda: Zakhala bwino

Mmodzi mwa atsogoleri a makomitiwo a Gladys Ganda ati ndi bwino kuti ndalamazo zayamba kubwezedwa koma adaonjeza kuti makomitiwo sakhala chete mpaka K750 miliyoni yonse itabwezedwa.

“Zakhala bwino kuti ndalamazo zayamba kubwezedwa koma sikuti basi takhutila ayi tikufuna ndalama zonse zibwezedwe kuti zigwile ntchito yake,” adatero a Ganda.

Unduna wa zamalidwe limodzi ndi kampani ya SFFRFM adalipira kampani ya ku Mangalande K750 miliyoni kuti kampaniyo ibweretse fetereza wa AIP koma mapeto ake kampaniyo idalephera kubweretsa fetelezayo.

Poyankha kulira kwa Amalawi omwe amadandaula za pulogalamu ya AIP ya chaka chino, mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera sabata yatha adachotsa omwe adali nduna ya zamalimidwe a Lobin Lowe ndi achiwiri awo a Madalitso Wirima Kambauwa.

Koma potsatira kulira kwa Amalawi komweko, Nyumba ya Malamulo idakhazikitsa makomiti oti afufuze momwe ndondomeko ya bizinesi ya pakati paundunawo, SFFRFM ndi kampani yaku Mangalandeyo idayendera.

Koma poyankha mafunso a makomitiwo, wapampando wa Board ya SFFRFM a Marjorie Maluwa Phiri ndi mkulu wakampaniyo a Richard Chikunkhuzeni adasemphana zonena pa momwe bizinesiyo idayendera.

A Phiri adauza makomitiwo kuti bizinesiyo siyidatsate ndondomeko ya boma podumpha nthambi yoona zogula ndi kugulitsa katundu wa boma ya PPDA komanso a ACB.

Pamalamulo, nthambi iliyonse ya boma isadagule katundu wa ndalama zambiri imayenera kudutsa ku PPDA komanso ACB koma apa, nthambizo zidadumphidwa ndipo zidangomva kuti bizinesi yachitika.

Koma a Chikunkhuzeni adauza makomiti omwewo kuti pasiteji yomwe ndalamazo zidaperekedwa ku kampani yakunjayo, PPDA ndi ACB sizimawakhudza chifukwa idali siteji yongopeza msika.

“Ndalamayo idangoperekedwa ngati chikole chabe koma sikuti idali siteji yofunika PPDA ndi ACB. Iwowa akadabweramobe mtsogolo mwake,” adatero a Chikunkhuzeni.

Ndipo poonekera ku makomitiwo Lachinayi A Lowe adati iwotu akungopwetekedwa chifukwa amafuna kuthana ndi anthu amene amadyera mphoto pankhani ya malonda a feteleza.

“Pali chimvano cha mavu kufuna kugwwetsa amene akufuna kuthana ndi zachinyengo zimene zimachitika pankhani ya feteleza. Ntchito ndaigwira ku undunawu komatu kadontho ka palafini kakhoza kusokoneza mgolo wodzala ndi madzi,” adatero.

Related Articles

Back to top button
Translate »