Nkhani

Chiyembekezo cha amalawi ku nyumba ya malamulo

Listen to this article

Pomwe aphungu a ku Nyumba ya Malamulo akuyamba mkumano wawo wounika bajeti ya 2022-2023 pa 14 November 2022, Amalawi ati mkumanowo ukabale mayankho a mavuto omwe akusefukira m’dziko muno.

Akadaulo komanso mafumu akuluakulu ati aphungu ali ndi udindo wounikira ndi kukonza pomwe zinthu zikupotoka m’dziko muno chifukwa Nyumba ya Malamulo n’chiwalo chimodzi chofunikira m’boma.

Gawo 6 la malamulo a dziko la Malawi limati nyumbayo ndiyo ili ndi mphamvu zopanga malamulo ndi kuunikira momwe boma likuyendera ndipo palibe nthambi ina yoposa mphamvuzo.

Wapampando wa mgwirizano wa magulu omenyera anthu ufulu a Gift Trapence ati mkumano omwe ukubwera pa 14 ndi mwayi waukulu wa aphungu owonetsa Amalawi kuti voti yawo idapita kwa anthu oyenera.

Iwo ati mmalo mwa mikangano, kujomba ndi nkhani zina zosafunikira kwenikweni zomwe zimataya nthawi, aphunguwo akapeze mayankho pa mavuto a zachuma, kusowa kwa mafuta ndi kusowa kwa ndalama zakunja.

“Kuonjezera apo, aphungu adzakhumudwitsa Amalawi akakapanda kukambapo kalikonse kokhudza pulogalamu ya AIP ndi ziyangoyango zomwe pulogalamuyo ikudutsamo. Amalawi akuyembekezera kuona Nyumba ya Malamulo yokhala mbali ya anthu,” atero a Trapence.

Pankhani yojomba kuzokambirana m’nyumbayo, Sipikala wa nyumbayo a Catherine Gotani Hara adachenjeza pamkumano watha kuti aphungu ojomba sazilandira alawansi ya tsiku lomwe ajombalo.

Paramount Chief Lundu ati Amalawi sadzakondwa ngati aphunguwo sadzakambirana nkhani ya chakudya, kusowa kwa mafuta, komanso momwe Amalawi angapezere ndalama zothetsera mavuto awo.

“Amalawi adakaponya voti kusankha aphungu owaimilira ndiye nthawi yakwana kuti nkhope yomwe adavoterayo ayione kudzera mumkumano umenewu. Kunjaku zinthu sizilibwino ndipo anthu maso ali ku Nyumba ya Malamulo,” atero a Lundu.

Mfumu yaikulu pakati pa Atumbuka a Paramount Chief Chikulamayembe ati mavuto omwe ali m’dziko muno ngofunika kuganiza mozama kuti angathe bwanji ndiye mpofunika kukambirana zakupsa.

“Mavuto omwe tili nawowa ngofunika njira zothana nawo mwatokha osadalira kuti ena ake abwera adzawathetse ndiye aliyese akakhala pansi azilingalira kuti yankho nchiyani,” atero a Chikulamayembe.

Ndipo mkulu wa bungwe loyimilira anthu ogula la Consumers Association of Malawi (CAMA) a John Kapito ati aphunguwo akuoneka kuti sadziwa kapena adaiwala mphamvu zomwe voti ya Amalawi idawapatsa.

A Kapito ati aphungu akadakhala kuti amamvetsetsa mphamvu zomwe ali nazo, sibwenzi mavuto ena omwe ali m’dziko muno alipo.

“Nyumba ya Malamulo pano idafowokeratu ndipo siyidziwa n’komwe kuti ikuyenera kupanga chiyani ndipo ikulowera kuti. Aphungu adaiwala kuti iwo ndiwo ali ndi mphamvu zambiri chifukwa adachita kusankhidwa kusiyana ndi nduna kapena adindo ena,” atero a Kapito.

Iwo ati aphungu ali ndi mphamvu zopanga malamulo okomera Amalawi kapena kuunika malamulo omwe akupweteka Amalawi pa nkhani zachuma ndi makhalidwe komanso kupereka ndalama komwe zikufunika kwambiri.

“Pano Amalawi akudutsa m’nyengo yowawa kwambiri chifukwa aphungu adamira n’kugawanika kwawo ndiye boma likungopanga zomwe laganiza chifukwa oyenera kuliunikira sadziwa udindo wawo,” atero a Kapito.

Iwo ati nthawi zonse aphunguwo akamakakumana nkhani imakhala imodzimodzi ya mtsutso pankhani zosapindulira anthu omwe adawapatsa mphamvu zokawaimilira ndipo nthawi zambiri amatsogoza zofuna zawo.

Mneneri wa nyumbayo a Ian Mwenye atsimikiza kuti aphunguwo ayamba kukumana pa 14 November 2022 koma poyankha funso la Tamvani Lachiwiri adati komiti yopanga ndondomeko ya zokambirana kunyumbayo idali isadakumane kuti ipange ndondomekoyo.

Related Articles

Back to top button