Kodi za Gaba zalowa?
M’sabatayi aganyu tidali osangalala kumva kuti chilombo cha ukonde, Gabadihno Mhango, mwana wa Flames, tsopano wayamba kusewerera m’timu yatsopano ya Bloemfontein Celtic.
Kuonetsa ukadaulo wake, chilombochi chidathandiza timuyi pofanana mphamvu ndi Moroka Swallows, pomwe masewerowo adathera 2-2 Gaba atachinya patangotsala mphindi ziwiri kuti masewero athe.
Kumeneku ndiye timati kubwera, ngakhale zina zimavuta mwanayu amatha kuwona ukonde.
Komabe tati tifunse ngati ndalama za mnyamatayu zalowa. Mmene adasewerera patsikuli zidaonetsa kuti sadapite pamtengo wolira.
Zimasonyezeratu kuti kukatamuka kulipo zikangolowa. Kodi zalowa zingati? Ena alankhulapo kuti popeza Gaba adapita monga wopanda timu ndiye kuti apita wabule.
Tikukhulupirira kuti awa ndi mabodza, paja Amalawi amakonda kumva zamabodza. Tikuyembekeza kuti zikalowa zinthu zisintha kukalabu.
Za bolera zili pati?
Moni kwa Nyerere, Jombo ya KB, Mabankers komanso Civo pamene ntchito ikuyambika lero ku Lilongwe m’chikho cha Standard Bank. Ena atuluka mmawa weniweni kuli mbuuu!
Komabe izo zili apo, aganyu tafuna timve za momwe bolera wotchedwa Solomon akupezera.
Mnyamata ameneyu adapondedwa ndi jombo mwezi wathawu koma kufika lero sizikudziwika momwe akupezera.
Aliyense wangoti ziii, kapena ndi zopanda ntchito? Malipoti akungoti wasiya kulankhula, ena ati wasiya kupita kusukulu. Monga aganyu tati tifuseko a Sulom kuti kodi munamuyendera mnyamatayu? Nanga ali bwanji?