Kuli ziii! za mapulaimale

Pamene ntchito ya kalembera wa chisankho cha pa 21 May 2019 walowa m’gawo lachinayi, zipani zandale zikuluzikulu zikadali duuu, osafuna kunena tsiku lomwe zidzachititse mapulaimale osankha amene adzaziimire pa uphungu ndi ukhansala.

Ndipo akadaulo ena a ndale ati kusachita mapulaimale msanga kumadzetsa mpungwepungwe pomwe anthu amene sanakhutire ndi zotsatira amaima paokha.

Pachisankho cha m’chaka cha 1994 palibe wodzambatuka m’chipani chake amene adapambana mwa aphungu 177 pomwe mu 1999, anthu anayi adapambana ataukira zipani zawo pa mapulaimale mwa aphungu 193. Ndipo mu 2004, odzambuka 38 adakalowa m’Nyumba ya Malamulo pomwe mu 2009, chiwerengerocho chidatsika kufika pa 32 ndipo mu 2014 odzambuka 52 adapambana.

Zipani za MCP ndi DPP mmbuyomu zidati zichititsa mapulaimale mwezi uno koma padakalipano zasintha thabwa.

Woyendetsa kampeni mu MCP, Moses Kunkuyu, adati chipanicho chidzachita mapulaimale mu November, mmalo mwa pa 20 August.

“Tasintha ndipo tidzachita mapulaimale ntchito ya kalembera wa ovota atatha mu November,” adatero Kunkuyu.

Mlembi wamkulu wa DPP Grezelder Jeffrey adati akuyesetsa kuti pa mapulaimale awo pasadzakhale kudzambuka monga mmbuyomu.

“Tikukambirana nawo nkhani zosiyanasiyana koma chachikulu tikuwalimbikitsa kuti azikopa anthu mwa mtendere ndi kuwalangiza kuti omwe adzalephere asadzadzimbuke koma kudzathandizana ndi omwe adzapambane,” adatero iye.

Mneneri wa UDF Ken Ndanga wati chipanicho chapanga kale ndondomeko yapamwamba yofuna kuti pasadzakhale kudzimbuka kulikonse mapulaimale akadzachitika koma nacho sichidabwere poyera kuti mapulaimalewo adzachitika liti.

“Mapulaimale adzakhala ochita kuponya voti yachinsinsi osati zoima kumbuyo kwa opikisana kuopa zosankhira mantha. Izi zidzatithandiza kuti pasadzakhale odzimbuka pamapeto,” adatero iye.

Mlembi wamkulu wa UTM Patricia Kaliati adati nkhani yaikulu yomwe imapinga ndi kulembetsa chipani yomwe yatha tsopano.

“Takonzeka. M’madera ena mukupezeka makandideti anayi kapena asanu omwe tikukumana nawo ndipo takondwa kuti ambiri akuvomera kuti akadzagwa, sadzadzimbuka koma kugwira ntchito ndi wopambanayo,” adatero iye.

Mneneri wa PP, Noah Chimpeni, adati akulimbana ndi nkhani ya konvenshoni yomwe akukonza kuti idzakhaleko pa 30 ndi 31 August mumzinda wa Blantyre.

“Nthawi siyinathe. Tikupanga chinthu chimodzi nthawi imodzi,” adatero iye.

Koma akadaulo a zandale Mustafa Hussein wa ku Chancellor College ndi George Phiri wa ku University of Livingstonia (Unilia) ati chidodo pa mapulaimale chingadzetse mavuto chifukwa kusokerera zigamba zodza ndi kudzimbuka kungavute.

Malinga ndi Hussein, mapulaimale a changu amathandiza kusankha atsogoleri a mphamvu chifukwa kukhala ndi nthawi yokwanira yowaonetsa kwa anthu.

“Mpikisano onse umayambira ku mapulaimale chifukwa ndiko anthu ndi chipani amasankha odzapikisana pachisankho chomaliza.

“Chipani chikakonzekera bwino n’kudzipatsa nthawi yokwanira yopanga mapulaimale, chimadzipatsa nthawi yokwanira yogulitsa odzawaimira,” adatero Hussein.

Phiri adagwirizana ndi Hussein ndipo adaonjezera kuti chipani chikapanga mapulaimale msanga, chimakhala ndi nthawi yokwanira yokambirana ndi odzimbuka kuti asathawitse anthu.

“Pampikisano pamakhala olephera ndithu ndipo mtima wodzimbuka umakhalapo koma chanzeru n’kukambirana nawo kuti asagawe anthu ndipo izi n’zotheka ngati pali nthawi yokwanira kutero,” adatero Phiri.

Iye adati kuti nthawi yotere ipezeke, mpofunika kupanga mapulaimale nthawi yabwino kuti chisankho chenicheni chisadafike, kusemphana konse kukhale kutalongosoledwa chipani chitamanga fundo imodzi.

Iye adatinso mapulaimale a changu amathandizanso chipani kuti chithe kupima bwino mphamvu zake m’madera osiyanasiyana pogwiritsa ntchito anthu omwe asankhidwa kudzachiyimira.

“Chipani chimakhala ndi nthawi yokwanira younika kuti kodi munthu wawoyo ali ndi anthu omutsatira ochuluka bwanji chifukwa nthawi zambiri, anthuwo amakhalanso mavoti a chipani ndiye mapulaimale safunika kufutsa ayi,” adatero Phiri.

Share This Post