Kupakula kukapitolo, JB achotsa nduna
Mtsogoleri wadziko lino Joyce Banda Lachitatu adakana kupumitsa mamulumuzana ena aboma kutsatira kupakula ndalama za boma kumene kwanyanya kulikulu la boma ku Lilongwe.
Polankhula kunyumba ya boma ya Sanjika pomwe amafika m’dziko muno kuchokera ku United States of America komwe adakagwira ntchito za boma, Banda adati sangachotse akuluakulu enawo, kuphatikizapo nduna ya zachuma Dr Ken Lipenga, mlembi wamkulu wa ofesi ya pulezidenti ndi nduna zake Hawa Ndilowe, chifukwa kufufuza kudakali mkati.
“Sindiikira kumbuyo aliyense chifukwa aliyense amene akukhudzidwa ndi nkhaniyi atengedwa. Padakali pano tikadali kufufuza. Wakubatu amakhala wakuba akagwidwa ndiye tisagwiritse ntchito mphekesera,” adatero Banda.
Nthawi yomwe amanyamuka m’dziko muno, n’kuti woyang’anira kayendetsedwe kachuma m’dziko muno Paul Mphwiyo ataomberedwa ndi mbanda zimene sizikudziwika. Sabata zapitazi apolisi akhala akugwira ogwira ntchito m’boma ena amene akhala akupezeka ndi mamiliyoni osololedwa kuboma. Ndipo anthu ena awiri adawagwira powaganizira kuti ndiwo adaombera Mphwiyo.
Banda ali ku America, anthu ena komanso mabungwe amati akangofika apumitse akuluakulu ena m’boma chifukwa alephera malinga ndi kubedwa kwa mipukutu ya ndalama.
Mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wa ogula la Consumers Association of Malawi (Cama) John Kapito amati pamene mphongozo zikupuma naye Banda apume nawo ponena kuti walephera.
Koma Banda adati: “Mfumu yabwino imaitana mbali zonse kuti zimverane chigamulo chisadapangidwe.”
Iye adati wakhazikitsa komiti yothana ndi umbanda imene ifukule chatsitsa dzaye kuti kusolola kukule kukapitolo, ndipo iye adati adazizwa pamene adamva kuti mabuku a kubanki a mtsogoleri wakale wa dziko lino Bingu wa Mutharika adapezeka kuti ali phwamwamwa ndi K61 biliyoni yosadziwika kochokera, zimene zidasonyeza kuti kusolola kudafika pena.
Zionetsero za Cama zidachitika mumzinda wa Lilongwe Lachinayi pamene Kapito ndi anthu ena adakapereka kalata yawo kukhonsolo ya mzindawo yomwe imapita kwa Banda.
Kalatayo idasenza mfundo zingapo koma zikuluzikulu kudali kukakamiza Lipenga kuti atule pansi udindo ndi kukakamiza Banda kuti aulule chuma chake.
“Tapereka masiku atatu kuti akhale atayankha apo ayi tizigona m’misewu,” adatero Kapito.
Banda adati kutsatira kusolola komwe kwachitika m’dziko muno, akumana ndi nduna zake kuti amve zingapo zomwe zidachitika.
Kukumanako amati kuchitika Lachinayi lapitali. Iye adati apanga chiganizo akalandira malipoti, kuyankha omwe amamupempha kuti atule pansi udindo.
Patsikulo Banda adati sadanene kuti akudziwa anthu amene adathira mpholopolo mkuluyo.
Izi zidabweza mawu amene Banda adanena pamsonkhano wa amayi achisilamu mumzinda wa Blantyre kuti akudziwa amene adathira machaka Mphwiyo.
“Sindidanene kuti ndikudziwa amene adaombera Mphwiyo, ndidati ndikudziwa cholinga cha amene adaombera Mphwiyo kuti akudana ndi ntchito yothetsa katangale yomwe boma langa likugwira,” adatero iye.
Pa nkhani youlula chuma chake komanso wachiwiri wake, Banda adati mwina anthu akumuumiriza kuulula chifukwa ndi wamkazi. “Kodi ena aja simumawafunsa bwanji? Kapena mukufunsa ine chifukwa ndine mayi?” adazizwa iye.
Iye adati akufuna aphungu akumane pofika November kuti akakambiraneko za bilo yokhudza kuulula chuma cha atsogoleri a dziko lino. Iye adati lamulo latsopano lidzaperekanso mphamvu kuti nduna ndi akuluakulu ena a boma, komanso a makampani omwe siaboma aziulula chuma chawo.
Banda adatinso lamulo latsopanolo lidzapereka mphamvu kwa Amalawi kufunsanso atsogoleriwo chuma chawo akamachoka m’boma.
Mtsogoleriyu yemwe mafunso ena amawadzeretsa kwa nduna zake kuti ziyankhe, adati anthu asadadandaule chifukwa boma lake layamba kunjata amene akukhudzidwa ndi katangale amene adayambika m’boma la UDF ndi DPP.