Nkhani

Kusiya ana akunjira muwilo

Sabata yathayi mmodzi wa awerengi a tsambali adafunsapo pankhani ya ana akunjira, makamaka mounikirapo pa zikalata zomwe makolo owabereka amasiya kulongosola momwe katundu wawo adzagawidwire akamwalira.

Kalatayo idali motere:

Rabecca, mchemwali wanga adapatsidwa pathupi ndi mwana wa mfumu ina mdziko muno. Awiriwa sadakwatirane koma bambo wa mwanayu ankamusamalira mwana wake munjira iliyonse kufikira bamboyo adamwalira.

Panthawi imene amamwalira bamboyo nkuti atalemba chikalata chofotokoza kuti chuma chake chonse chikhale cha mwana yemwe adabereka ndi mchemwali wangayo.

Koma makolo a bamboyo adakana kuvomereza zolembedwa mkalatayo akuti chifukwa mwanayo adali obadwira kunjira. Mchemwali wanga wayesa kupita kupolisi komanso kwa bwanamkubwa wa boma lomwe amakhala koma sizikuphula kanthu.

Mchitidwe wa banja la mfumuyi ndilopatsa mwanayu umphawi pomwe adali ndi kholo lomwe lidakonzekera bwino za kaleledwe ka mwana wake.

Komanso ichi ndi chitsanzo chabe cha mavuto omwe ana obadwira kunjira akukumana nawo makolo awo akamwalira chifukwa kawirikawiri anawa sawerengedwa pamodzi ndi ana ena kapena abale omwe amayenera kulandirapo kangachepe kuchokera pachuma cha kholo lawo lomwalira, pamene chikhalirecho kholo lili moyo limawathandiza ana aja.

Choncho kumumana mwana gawo la chuma cha kholo lake nkulakwira komanso kuzunza munthu wosalakwa chifukwa mwana sasankha kuti abadwe pabanja kapena ayi. Izi ndi zisankho za makolo.

Nthawi zina zimatha kuvuta bambo wa mwanayo akamukana, koma munkhani yakwathuyi munthu amene adabereka mwanayo adavomereza kuti mwanayo adali wake ndipo nthawi yomwe adali moyo adamusamalira mmene kholo lililonse lingayang’anire mwana wake.

Kupyolera apo, kholo la mwanayo lidachiona choyenera kuti mwanayo asiyiridwe chuma choti chimuthandize bamboyo ali kuli chete.

Koma motsutsana ndi zofuna za malemuyo, achibale ena adasankha kuti mwanayo asalandire kanthu pomuweruza kuti ndiwosayenera kutero pokhala kuti sadabadwire m’banja.

Kodi moyo wamwana kapena zofuna zake zingakhale zoperewera chifukwa choti wabadwira kunja kwa ukwati? Nzoona kuti mwanayu amanidwe chuma chifukwa chakuti ndiwakunjira?

Anthu omwe akudya chumacho lero ngoyenerera bwanji kupindula poyerekeza ndi mwanayu yemwe akusoweka chithandizo kuti aphunzire komanso kukula bwino?

Awerengi ena mukuonapo bwanji pamenepa?

Related Articles

Back to top button