Kutakata ndi ulimi wa mitengo ya zipatso
Pamene alimi ena akukangalika ndi ulimi wa ziweto kapena mbewu zina, Pilirani Tendai Khoza adapeza mtaji pa ulimi wa mitengo ya zipatso. Mlimiyu yemwe ndi mwini komanso mkulu wa Phiko Farms m’boma la Lilongwe akufotokoza zambiri za ulimiwu. ESMIE KOMWA adacheza naye motere:
Choyamba mungotidziwitsa kuti phiko farms imapanga chiyani?
Pikho Farms imapanga ulimi wogulitsa mbande za mitengo ya zipatso monga mango, mpesa, mapichesi, malalanje, manachesi, maapulo, mapeyala, mapapaya, ma nectaren, mapulamu, magalagadeya ndi zina zambiri.
Mbewuzi ndi zocha msanga ndipo zimabereka pasanathe chaka. Ubwino wina wa mitengoyi ndi woti zipatso zake zimakhala zokoma ndi zofewa kusiyana ndi zamakolo.
Nanga munayamba liti ulimiwu?
Ulimi umenewu ndidayamba m’chaka cha 2012 pamene ndimachita ukachenjede wanga ku Bunda.
Kodi chidakuchititsani kuti muyambe ulimiwu ndi chiyani?
Ulimiwu ndidayamba kalekale ndili mwana.
Ndikukumbukira kunyumba ndinali ndi kadimba kuseli kwa nyumba ya kwathu koma nditapita kusekondale ndinasiya.
Ndinakayambiranso nditapita kusukulu ya ukachenjede ndili chaka chachiwiri. Nyengo imeneyo ndi imene mayi anga adali atamwalira kumene ndipo ndidayamba ulimi wamadimba kuti ndizidzithandizira.
Ndinayamba kulima ndiwo zamasamba mpaka kukula pano ndimalima mitengo ya zipatso.
Nanga luso lopanga mbandezi mudalipeza kuti?
Luso limeneli ndidaliphunzira kwa anthu ena malingana ndi chidwi chimene ndinali nacho.
Sindinganene kuti ndinaziphunzira m’kalasi ayi chifukwa lusoli limapezeka m’pulogalamu ya ulimi wa zipatso pamene ine ndinachita maphunziro a zankhalango ndi chilengedwe.
Kuyenda m’maiko ambiri ndi kumene kunapangisa kuti ndiphunzire zinthu zambiri zokhudzana ndi ulimiwu.
Nanga mbewu yopangira izi mumaipeza kuti?
Monga ndanena, ndayenda ndithu maiko angapo ku Africa kuno, ku America, ku Mangalande komanso ku Ulaya choncho mbewu ndazitengapo m’maiko osiyanasiyana.
Kodi mbande zanu zimasiyana bwanji ndi za alimi ena?
Choyamba ife mitengo yathu ndi yakolite komaso yambiri ndiyoti ku Malawi kuno kulibe monga ndanena kale kuti ndatengapo mitengo m’maiko angapo.
Chachiwiri ife ndi achilungamo pantchito yathu. Mwachitsanzo, munthu tikamuuza kuti uwu ndi mtengo wa malalanje zipatso zimakatuluka zomwezo ndithu pamene mavenda ena amakugulitsa mandimu kunama kuti ndi malalanje.
Kuonjezera apo, timapereka ukadaulo mwaulere kwa makasitomala athu mmene angasamalilire mitengoyo chifukwa tili ndi ukadaulo wakuya.
Kodi ulimiwu ndi wopindulitsa?
Ulimi ulionse ngopindulitsa, wasiyana ndi mabizinesi ena chifukwa tsiku lililonse munthu amayenera adye ndiye amayenera kugula ndithu komanso ulimi wa zipatso ku Malawi kuno sitinayambepo.
Tangoganizani kufikira lero tutengabe maapulo ku Joni chonsecho nthaka yathu ndi yolola chilichonse koma zimangofunikira upangiri wabwino.
Nanga mungafotokoze mwachidule mmene mumapangira mbande zanu?
Mbande zathu timapanga kudzera m’kukwatitsa.
Pali njira zingapo zokwatisira mbande kuti zituluse zipatso zokoma ndi zocha msanga koma zikufunika kalasi yapadera kuti ndilongosole mwachindunji.
Kodi ndi mavuto anji amene mumakumana nawo ku ulimiwu?
Pa ulimi ulionse pamakhala nthawi yoti mwina kugwa zirombo ndi kuononga mbewu ndiye timayenera kuti tipeze mankhwala othana nazo.
Nthawi zina akuba amaba mitengo panazale koma kwambiri vuto limakhala kusowa misika ikuluikulu monga kugulitsa ku boma zimakanika moti sitidziwa kuti anthu amene amapeza mwayi wotere amatani chifukwa mitengo yathu ndi yabwino komanso yocha msanga.
Vuto lina ndi loti anthu sakuzindikirabe kuti nthaka yathu imalola chilichonse. Mwachitsanzo, tidakaganizabe mwachikale kuti mpesa ku Malawi sachita bwino koma ku South Africa.
Nanga masomphenya anu ndi otani ku ulimiwu?
Ndimafunitsitsa kuti nthawi idzakwane yoti Malawi izidzazilimira zipatso yokha osati ndi ma orange omwe kumatenga m’maiko a eni ayi chonsecho kuthekera tilinako amalawi.
Mawu anu omaliza ndi otani?
Zipatso monga maapulo, mpesa kaya mapulamu ali ndi uthekera kochita bwino m’dziko muno ndipo umboni tili nawo.
Bwerani mudzagule mbande zathu ndipo tidzakuphunzitsani ukadaulo wake kuti mutulutse zipatso zapamwamba zimene zimachokera m’maiko abundance. n
Mukafuna kulumikizana nawo aimbireni foni pa 0888 160 201