Nkhani

Kwafa bulu ku DPP

Mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) a Peter Mutharika wauza mamembala omwe sakumumvera m’chipanicho kuti achoke asaononge chipani.

A Mutharika adalankhula izi Lachitatu lapitali pamsonkhano omwe adakonza wa komiti yaikulu ya chipani ku Nkopola Lodge m’boma la Mangochi potsatira zomwe akuluakulu ena akhala akuchita monga kupangitsa msonkhano wina wa komiti yaikulu.

Adadzudzula osokoneza chipani: A Mutharika

Mlembi wamkulu wa chipani cha DPP a Grezelda Jeffrey adachititsa msonkhano wa komiti yaikulu ku Lilongwe Lachitatu sabata yatha komwe mwa zina adakonza msonkhano okasankha adindo mumzinda wa Lilongwe koma a Mutharika kudzera kukhothi adaletsa zomwe msonkhanowo udagwirizana.

A Mutharika adzudzula mmodzi mwa akuluakulu omwe akufuna utsogoleri wa chipanicho a Kondwani Nankhumwa kuti aonongetsa ndalama za chipani kulipira maloya pa nkhani zopanda pake. “Ndipo ndikudabwa kuti ngati anthu ena m’chipanichi amachikonda n’chifukwa chiyani akukhalira kukhothi kukatenga ziletso? Taononga ndalama zambiri kulipira maloya pankhani zopepela chifukwa cha anthu ngati amenewo,” atero a Mutharika.

Koma Lachinayi, a Nankhumwa  omwe adawachotsa pa mpando wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipanicho m’chigawo cha kummwera ndi kuwasankha kukhala mlangizi wa a Mutharika wati walandira ganizo la msonkhano waukulu umene ukukonzedwawo.

“Zikuoneka kuti a Mutharika avomereza kufunika koti chipanicho chichititse msonkhano waukulu pasanafike pa 29 December monga bwalo lidalamulira. Zakhalanso bwino kuti a Mutharika anena poyera kuti akufuna kudzaima nawo popikisana kwa amene adzaimire chipanicho pa chisankho cha 2025,” adatero a Nankhumwa m’chikalata chawo.

A Mutharika adakalipiranso a Ken Msonda kuti iwo ndi alendo m’chipanicho ndipo wati ngati atopa abwerere kuchipani chawo cha People’s Party (PP) komwe adachokera.

“A Msonda mwakhala mukundinyoza koma ndimangokusiyani koma ndikukumbutseni kuti inuyo ndi wobwera m’chipanichi mudali ku PP ndipo ngati mwatopa bwererani ku PP musationongere chipani,” atero a Mutharika.

Iwo ati ali n’chikhulupiriro kuti chipani chawo chidzabwera m’boma m’chaka cha 2025 chifukwa Amalawi azindikira kuti adalakwitsa posintha boma pachisankho chobwereza cha 2020 koma pano akonzeka kudzakonza zinthu. 

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button