Nkhani

Ziphaso zitheka pofika 2025

Listen to this article

Nduna ya za chitetezo cha m’dziko a Ken Zikhale Ng’oma ati pofika m’chaka cha 2025 pomwe Amalawi adzaponye voti ya adindo, m’Malawi aliyense woyenera kuponya voti adzakhala ndi chiphaso cha unzika.

Chiphaso cha unzika ndi umboni okhawo omwe anthu m’Malawi muno akhoza kuloledwa kuponya voti koma aphungu a m’maboma a kummwera akhala akudandaula kuti m’chigawocho zitupa zikuvuta kutuluka.

A Ng’oma ati vuto lomwe lidalipo la kuchepa mphamvu kwa makina otulutsa zitupa latha chifukwa boma lagula makina ena amakono komanso likukonzetsa makina ena akale omwe adaonongeka.

“Imeneyo isakhale nkhawa yanu, panopa tagula makina ena owonjezera omwe azitulutsa zitupa 2 500 patsiku ndiye osakhala ndi nkhawa chifukwa pofika 2025 aliyense wofunika chitupa adzakhala nacho,” atero a Ng’oma.

Phungu wa Nyumba ya Malamulo ku Thyolo South West a Chimwemwe Chipungu ati m’madera ambiri kummwera anthu akuvutika kuti apangitse kapena kubwezeretsa zitupa sakutha.

“Tikumva kuti m’zigawo zina anthu akupangitsa zitupa kapena kubwezeretsa mosavuta koma kwathuku kummwera tikumva mavuto osiyanasiyana ena osamveka n’komwe,” atero a Chipungu.

Nkhawa yawo yagwirizana ndi nkhawa ya phungu wa pakati m’boma la Thyolo a Ben Phiri omwe adati nthawi nthambi yopereka zitupa ikuyenera kukhala ndi maofesi kufupi ndi anthu.

A Phiri ati ndondomeko ya pano, anthu amayenera kukatengera zitupa kuofesi ya bwanamkubwa ndiye potengera mtunda okafika kumeneko anthu ambiri amagwa ulesi.

“Bwanji osakhazikitsa maofesi kwa ma T/A kapena mafumu akuluakulu kuti anthu azikatengera zitupa kumeneko? Nthawi zinatu zitupa zimatuluka koma munthu wa kumudzi akaganizira mayendedwe pamavuta,” atero a Phiri.

A Ng’oma ati maganizowa ngomveka koma akakambirana ku unduna kuti aone zomwe angachite chifukwa ndi nkhani yokhudza malamulo ndi ndondomeko za boma.

Koma iwo adati anthu omwe ali ndi zitupa zakutha asade nkhawa chifukwa zikuloledwa kugwira ntchito mpaka chaka cha 2026 kutanthauza kuti akhoza kudzagwiritsa ntchito poponya voti.

“Musadandaule kalikonse, palibe kusokonekera kulikonse pachisankho, oyenera kuponya voti adzaponya amenewo ndiye mawu anga ndipo mukhulupirire,” atero a Ng’oma.

Mneneri wa bungwe loyendetsa zisankho la MEC a Sangwani Mwafulirwa ati bungwero lidzapereka mpata wofanana kwa aliyense yemwe akuyenera kudzaponya voti osatengera boma kapena chigawo.

Related Articles

Back to top button