Chichewa

Kwaterera ku DPP

Listen to this article

Madzi achita katondo kuchipani cha Democratic Progressive Party (DPP) chomwe chidali m’boma kwa zaka 6 zapitazo ndipo chidagwetsedwa ndi m’gwirizano wa Tonse Alliance pachisankho chobwereza cha pa 23 June 2020.

Lachinayi lapitali anthu adadzidzimuka ndi kuchotsedwa kwa mlembi wamkulu wachipanicho Greselder Jeffrey yemwe mtsogoleri wa DPP Peter Mutharika adamuchotsa popanda msonkhano waukulu wachipani.

Jeffrey adachotsedwa pampandowo atauza nyuzipepala ya The Nation kuti chipanicho chikufunika msonkhano waukulu wokasankha atsogoleri ena makamaka pulezidenti, chifukwa Mutharika wapangako mbali yake.

Mmbuyomu zinthu zikuyenda: Mutharika kupatsana moni ndi Greselder

Mutharika adatsogolera DPP pachisankho cha 2014 chomwe DPP idachotsa People’s Party (PP) m’boma, Mutharika yemweyo adaimira DPP pachisankho cha 2019 chomwe chidakanidwa atapambana kenako adagwetsa chipanicho pachisankho chobwereza cha 2020.

Pazisankho zonse ziwiri cha 2019 ndi 2020, Jeffrey ndiye adali mlembi wamkulu wachipanicho.

Polankhula ndi The Nation Lachitatu, Jeffrey yemwe adakana kuti sachoka pampandowo adati iye aonetsetsa kuti msonkhano waukulu wachipani uchitike.

“Anthu m’chipani akufuna msonkhano waukulu chifukwa akuona kuti ndi njira yokhayo yokonzera chipani. Sindichoka ndikhala m’chipani ngati mlembi wamkulu sindikupita kulikonse,” adatero iye.

Akadaulo pa ndale ayikira kumbuyo Jeffrey kuti akutsata ndondomeko yoyenera ya demokalase pofuna kuti adindo azisankhidwa ndi anthu a m’chipani osati munthu mmodzi chifukwa chotenga chipani ngati chake.

Rafiq Hajat wati chipani cha DPP chikufunika msonkhano waukulu kuti chibwezeretse chikhulupiriro mwa Amalawi.

“Vuto lomwe lilipo ndi loti zipani za m’Malawi muno zimakhala ngati chuma cha munthu kapena banja ndiye za demokalase sawerengera amafuna mwini wakeyo ndiye azinena zochita. Ichi n’chifukwa chake zipani zambiri zimafa mosadziwika,” watero Hajat.

George Phiri wa kusukulu ya ukachenjede ya  University of Livingstonia wati popanda msonkhano waukulu, chipani cha DPP chikhoza kudzibaya chokha kumsana chifukwa chikupereka uthenga wolakwika kwa Amalawi.

“Uthenga omwe akupereka ndi woti safuna kumva za anthu. Ngati sadakonzeke za msonkhano waukulu akadangonena mmalo mochita kuonetsa kuti sakufuna msonkhano omwe uli m’malamulo a chipani chawo,” watero Phiri.

Naye Ernest Thindwa wa ku Chancellor College wati pafikapa, Mutharika akadangovomereza kuti wakula ndipo akuyenera kusiya chipani m’manja mwa omwe ali ndi mphamvu zoyendetsera.

“Mutharika amayenera kudziwa kuti mbiri ya chipani idaipa pautsogoleri wake ndiye zokakamiza izi siziwapindulira ayi,” watero Thindwa.

Lachinayi lapitali, komiti yaikulu ya DPP imakumana kunyumba kwa Mutharika ku Mangochi koma Jeffrey adati Mutharika adamuletsa kukakhala nawo pamsonkhanowo ngakhale udindo wake umamuyenereza kukhala m’komitiyo.

Aka si koyamba kuti chipani cha DPP chisemphane ndi akuluakulu ena chifukwa chodzudzula Mutharika kuti wakula ndipo asiyire ena mpando kuti apitirize. 

Related Articles

Back to top button