Nkhani

 Liwu la mafumu pa zochotsa anthu 1 miliyoni mu AIP

Listen to this article

Mafumu apereka maganizo osiyanasiyana pa ganizo la boma lochotsa maina 1 miliyoni mu pulogalamu ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo ya AIP.

Mlembi wa unduna wa za malimidwe a Dixie Kampani sabata yatha adatsimikizira nyuzipepala ya The Nation kuti chaka chino alimi a AIP akhala pakati pa 1.3 miliyoni ndi 1.5 miliyoni kuchoka pa 2.5 miliyoni.

Koma mfumu Kawinga ya ku Machinga ati boma likachita izi, liutsira mkwiyo mafumu chifukwa anthu ali ndi maganizo woti mafumu ndiwo amapereka maina choncho kuchotsa anthu oti adali kale pamndandanda kudzetsa udani.

Iwo ati kuonjezera apo, zichititsa kuti vuto la njala likule chifukwa anthu 1 miliyoni omwe achotsedwewo akhoza kudzakolola pang’ono kapenanso osakolola kumene chimene chizachititse vuto la kusowa kwa chakudya kuzakule.

“Chomwe chimachitika n’choti m’banja ngati muli anthu 10 koma tsiku limenelo mupezeke chakudya cha anthu atatu ndiye kuti anthu 7 akhala ndi njala ndiye amayang’anira kwa makolo omwe ndifeyo mafumu,” atero a Kawinga.

Nayo mfumu Mazengera ya ku Lilongwe inati boma lidakasintha ganizoli chifukwa alimi ambiri m’dziko muno ndi ang’onoang’ono omwe amadalira pulogalamu ya AIP kotero kuchotsa alimi 1 miliyoni kukolezera njala.

Iwo ati potengera momwe mtengo wa fetereza udakwerera, mpovuta kuti alimi ang’onoang’ono athe kugula paokha popanda ambiri mwa iwo salima mokwanira.

“Nkhani imeneyo t i d a i m v a k o m a chodandaulitsa n’choti pulaniyo yabwera nthawi yolakwika pomwe fetereza adakwera mtengo komanso ndalama ikuvuta kupeza,” atero a Mazengera.

Koma mfumu Mabilabo ya ku Mzimba inati mpofunika kulipatsa mpata boma kuti ligwiritse ntchito ndondomeko yomwe lakonza chifukwa zithandiza kuti magulu osiyanasiyana apindule nawo.

“Ngati mukulimvetsetsa boma, pulani ndi yoti anthu akhale m’magulu kuti ena agule zipangizo za makuponi. Ndiye pali ena a mtukula pakhomo ndi ena akuthekera kochita ulimi waukulu omwe akuwaika pa Agricultural C o m m e r c i a l i s a t i o n (Agcom).

“Izi zithandiza chifukwa kale lija ena amapezeka m’makatigole onse okha komanso ena amalandira makuponi pomwe sangathe kulima chifukwa cha ukalamba kapena ulumali kapenanso kusowa malo ndiye amenewa m’kumva kwanga alowa m’makatigole ena,” atero a Mabilabo.

Pulezidenti wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) a Manes Nkhata ati n’zomvetsa chisoni kuti mwa alimi 3 miliyoni oyenera kuthandizika mu AIP, theka lawo ndilo lithandizike chaka chino, kutanthauza kuti ambiri adakali m’goli la njala.

“Vuto loyamba ndi loti alimi ambiri adalandira fetereza mochedwa dzinja lathali zomwe zidachititsa kuti ambiri asakolole moyenera.

“Vuto lachiwiri ndi loti mtengo wa fetereza udakwera kwambiri kutanthauza kuti alimi 1.5 miliyoni otsalawo ayenera kugula fetereza odulayo zomwe n’zokaikitsa ngati angakwanitse,” adatero a Nkhata.

Koma a Kampani adati zonse zitengera kuti boma liika fetereza wa AIP pa mtengo wanji ndipo akapanga masamu ndi bajeti ya chaka chino apeza chiwerengero chenicheni.

“ C h i w e r e n g e r o chomaliza chidzatuluka boma likadzakhazikitsa mtengo wa fetereza wa AIP koma tikuyembekezera pakati pa alimi okwana 1.3 miliyoni ndi 1.5 miliyoni mu pulogalamu yachaka chino,” adatero a Kampani.

Panthawi ya kampeni, mgwirizano wa Tonse Alliance unkalonjeza fetereza otsika mtengo kwa aliyense(Universal subsidy) pa mtengo wa K14 500 ndipo m’chaka chake choyamba, alimi okwana 3.7 miliyoni adapindula.

Kuchoka apo, m’chaka chotsatira cha 2022/2023 chiwerengerocho chidatsika kufika pa 2.5 miliyoni ndipo pano mpomwe pabwera ganizo lotsitsanso chiwerengero kufika pa 1.5 miliyoni.

Related Articles

Back to top button