Nkhani

Boma likugwiritsa K3 biliyoni pothandiza ochotsa mimba

Dziko la Malawi likugwiritsa ntchito pafupifupi K3 biliyoni pa chaka popereka thandizo kwa amayi amene anachotsa mimba pogwiritsa ntchito njira zosatetezeka, watero m’modzi mwa madotolo a za ubereki a Francis Makiya.

Polankhula pomwe bungwe la Centre for Solutions Journalism (CSJ) linachititsa maphunziro a atolankhani pa nkhani zokhudza kuchotsa pathupi, a Makiya adati zipatala za boma zimalola kuthandiza amayi amene anachotsa mimba m’njira zosavomerezeka.

“Ngakhale malamulo amaletsa kuchotsa mimba, amayi ena amatero pa zifukwa zosiyanasiyana. Ena amakhala kuti akuopa kuti maphunziro athera panjira, mwina mimbayo si ya amuna awo kapena akuopa kutonzedwa komanso ena amaopa kutumbiza. Kukhala ndi malamulo okhwima si kutanthauza kuti izi sikukuchitika. Tikaona pa dziko lonse, maiko amene ali ndi malamulo okhwima ndi kumene amayi amachotsa mimba mosaziteteza,” iwo adatero.

A Makiya, omwe ndi mlembi wamkulu wa bungwe lothana ndi kuchotsa mimba mosatetezeka la Coalition for the Prevention of Unsafe Abortion adati n’zovuta kuti amayi omwe amachotsa mimba mosayenera pogwiritsa ntchito mitengo ya chinangwa kapena nsatsi, masipokosi, mabotolo a galasi ngakhalenso mankhwala ena a ku chipatala amapita ku chipatala komwe amathandizidwa.

“Ngakhale zikudziwika kuti amene achotsa mimba makamaka m’zipatala zomwe si zaboma amagwiritsa ntchito ndalama yosaposa K20 000, n’zovuta kuti amayi amene anachotsa mimba m’njira zosatetezeka amagwiritsa ntchito ndalama zingati kuti athandizidwe kuchotsa zotsalira m’zipatala za boma chifukwa zimatengera kuti mimba inali pati nanga avulala motani. Chinanso chimene ambiri sitiwerengera ndi nthawi imene amayi akhala m’chipatala kuti athandizidwe,” adatero iwo.

Malinga ndi kafukufuku a m e n e b u n g w e l a Guttmacher mogwirizana ndi sukulu ya madotolo ya College of Medicine adachita mu 2014, amayi a zaka za pakati pa 6 ndi 18 mwa 100 amene ali ndi pathupi, amamwal ira kaamba kofuna kuchotsa pathupipo. Malinga ndi kafukufukuyo, amayi 141 000 adachotsa mimba m’chaka cha 2015 ndipo 60 mwa amayi 100 amene adachotsa mimbawo adakalandira thandizo m’zipatala za boma.

K a f u k u f u k u akusonyezanso kuti mwa amayi 100 alionse amene adachotsa mimba m’njira zosatetezeka, 64.4 adali okhala m’madera a kumudzi. Potengera maphunziro, 12.1 mwa 100 alionse adaphunzirapo ku pulaimale, 54.3 mwa 100 adalowapo m’kalasi za secondale pomwe 33.6 adapitirira apo.

Potengera chipembedzo, amayi 74.4 mwa 100 alionse a Chikhristu, amayi 10.3 a Chisilamu ndipo 14.6 ndi a zipembedzo zina pomwe 0.7 alibe chipembedzo.

Mkulu wa bungwe la CSJ a Brian Ligomeka adati ambiri amanena kuti mabungwe ndi omwe akufuna kuti lamulolo lisinthe ndi kulingana ndi momwe lilili m’dziko la Zambia koma zoona zake n’zoti Malawi Law Commission ndilo lidapempha zoti lamulo lisinthe litachita kafukufuku pakati pa Amalawi osiyanasiyana.

“Ena mwa amene adasainira kuti lamulo litasintha ndi mabungwe a zipembedzo zikuluzikulu m’dziko muno ndi mafumu. Chonchotu iyi si bilo ya mabungwe koma nthambi ya boma,” adatero iwo.

ambiri mwa iwo salima mokwanira. sabuside m’malo mwake

“Nkhani imeneyo t i d a i m v a k o m a chodandaulitsa n’choti pulaniyo yabwera nthawi yolakwika pomwe fetereza adakwera mtengo komanso ndalama ikuvuta kupeza,” atero a Mazengera.

Koma mfumu Mabilabo ya ku Mzimba inati mpofunika kulipatsa mpata boma kuti ligwiritse ntchito ndondomeko yomwe lakonza chifukwa zithandiza kuti magulu osiyanasiyana apindule nawo.

“Ngati mukulimvetsetsa boma, pulani ndi yoti anthu akhale m’magulu kuti ena agule zipangizo za makuponi. Ndiye pali ena a mtukula pakhomo ndi ena akuthekera kochita ulimi waukulu omwe akuwaika pa Agricultural C o m m e r c i a l i s a t i o n (Agcom).

“Izi zithandiza chifukwa kale lija ena amapezeka m’makatigole onse okha komanso ena amalandira makuponi pomwe sangathe kulima chifukwa cha ukalamba kapena ulumali kapenanso kusowa malo ndiye amenewa m’kumva kwanga alowa m’makatigole ena,” atero a Mabilabo.

Pulezidenti wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) a Manes Nkhata ati n’zomvetsa chisoni kuti mwa alimi 3 miliyoni oyenera kuthandizika mu AIP, theka lawo ndilo lithandizike chaka chino, kutanthauza kuti ambiri adakali m’goli la njala.

“Vuto loyamba ndi loti alimi ambiri adalandira fetereza mochedwa dzinja lathali zomwe zidachititsa kuti ambiri asakolole moyenera.

“Vuto lachiwiri ndi loti mtengo wa fetereza udakwera kwambiri kutanthauza kuti alimi 1.5 miliyoni otsalawo ayenera kugula fetereza odulayo zomwe n’zokaikitsa ngati angakwanitse,” adatero a Nkhata.

Koma a Kampani adati zonse zitengera kuti boma liika fetereza wa AIP pa mtengo wanji ndipo akapanga masamu ndi bajeti ya chaka chino apeza chiwerengero chenicheni.

“ C h i w e r e n g e r o chomaliza chidzatuluka boma likadzakhazikitsa mtengo wa fetereza wa AIP koma tikuyembekezera pakati pa alimi okwana 1.3 miliyoni ndi 1.5 miliyoni mu pulogalamu yachaka chino,” adatero a Kampani.

Panthawi ya kampeni, mgwirizano wa Tonse Alliance unkalonjeza fetereza otsika mtengo kwa aliyense(Universal subsidy) pa mtengo wa K14 500 ndipo m’chaka chake choyamba, alimi okwana 3.7 miliyoni adapindula.

Kuchoka apo, m’chaka chotsatira cha 2022/2023 chiwerengerocho chidatsika kufika pa 2.5 miliyoni ndipo pano mpomwe pabwera ganizo lotsitsanso chiwerengero kufika pa 1.5 miliyoni.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button