Nkhani

Love ya pa Zed ikutipweteka

Listen to this article

La 40 lakwana. Zochitika ku Zambia komwe Flames imakapikisana nawo mumpikisano wa Cosafa zadziwika. Kumeneko Flames idataya bomwetamweta koma ati idatenga mapointi onse kwa mahule.

Asungwana a pa Zed tidatenga malo kumeneko ati mpaka kukwera nawo basi ya Flames uko akuyamikira anyamatawa ndi makochi kuti amasewera bwino. Timaganiza kuti poti akwera nawo basiyo ndiye kuti mphunzitsi wa Flames akawaseweretsa koma ife osawaona m’galaundi. Kodi adawaseweretsa malo ati?

Ndiyetu ta ku Zambia timachita kusangalala kuti na love ya ise tizapasa waneba osati wakawalala wapa Zed awa oyenda okha mukoshi opanda na kamusungwana kamushemushe ngati ise. Manje ma boys wapa Zed wali stingy kuposa wapa Malawi ka.

Aliyense inde atha kukopeka ndi tasungwana ta pa Zed komabe tikuganiza kuti nthawiyi idali yolakwika kuti tisamale osewera athu ngakhalenso makochi. Makochi ndi osewera ali ndi nthawi yambiri yongokhala, bwanji osapita kumeneko ndikukathana ndi tiasungwanati? Kodi masiku anayi akugwira ntchito ya dziko angalephere kupirira?

Anyamatawa amagwiritsira misonkho yathu kotero tikufuna chilungamo chioneke apa. FAM ndiyo mutu kuti atiuze zenizeni aganyu tisanaganize mopenga.

Uncle Tom adasiya osewera 7 ati amasowa khalidwe koma ena omwe adafuntha kumeneko adawatenga ku Rwanda. Kodi pali chilungamo apa?

Tipemphe kuti anthu omwe adali kumeneko atiuze chilungamo ndipo FAM isakhalire chilungamochi. Pamene tikusangalala kuti tagwetsa Rwanda kwawo, tikukhulupirira chisangalalochi chitidziwitsanso zoona zake.

Related Articles

Back to top button