Nkhani

‘Mafumu akusunga zitupa za ena’

Listen to this article

Pamene gawo lachitatu la kalembera wa chisankho cha pa 21 May 2019 akuyembekezeka kutha mawa m’boma la Lilongwe, anthu ena adandaula kuti akulephera kulembetsa chifukwa mafumu akusunga ziphaso zawo.

M’madera ena omwe Tamvani adazunguliramo, ena adandaula kuti mafumu adawalanda ziphaso za unzika ndipo akupereka ndalama kuti awabwezere zitupazo popita kokalembetsa pomwe m’madera ena akuti anthu akulephera kukalembetsa chifukwa cha miyambo.

Zopingazi zaululika pomwe zipsinjo zimene zidalipo m’gawo loyamba ndi lachiwiri makamaka zokhudza kuvutavuta kwa zipangizo ndi kamemedwe ka anthu zikuoneka kuti zakonzedwa.

Anthu pamalo olembetsera a Malembo kwa T/A Khongoni m’bomali Lolemba adati akulephera kukalembetsa chifukwa zitupa zawo za unzika

zili ndi mafumu omwe akufuna ndalama kuti awabwenzere zitupazo.

M’ndondomeko ya kalembera wa ulendo uno, bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) likugwiritsa ntchito chitupa cha unzika chokha ngati umboni woti munthu alembetse m’kaundula ndipo popanda chitupachi, munthu sakuloledwa kulembetsa.

Mmodzi mwa anthuwo, Moses Phiri, wa m’mudzi mwa Salamba adati mafumu adatenga zitupazo ati pofuna kulongosola za kaundula wa sabuside.

“Mafumu ndi a zamalimidwe adatenga kuti apangire kaundula wa makuponi a sabuside koma akuti pali chikonzero choti mudzi ulionse upereke ndalama yopangira kaundulayo ndiye tikupereka ndalama kwa amfumu kuti akulembe kenako n’kukubwezera chitupa chako,” adatero Phiri ataombola chitupa chake ndi K500.

Woyang’anira malo olembetserawo Ezala Nacford adatsimikiza kuti zitupa za anthu ambiri zili ndi mafumu zomwe zikupangitsa kuti anthuwo azilephera kulembetsa.

“Tabweza mafumu angapo atabwera ndi zitupa zambirimbiri kuti adzalembetsere anthu. Malamulo salola izo. Titafufuza, tapeza kuti eni zitupazo akulephera kukazitenga chifukwa sakupereka ndalama,” adatero Nacford.

Woyang’anira za zisankho ku bungwe la MEC Sammy Alfandika Lachiwiri adati kusunga chitupa cha wina ndi mlandu ndipo adachenjeza kuti aliyense yemwe ali ndi chitupa cha mnzake akuyenera kubweza.

“Aliyense ayenera kusunga yekha chitupa chake chifukwa chingafunike nthawi iliyonse osati ya kalembera yokha,” adatero Alfandika.

T/A Khongoni adadabwa atamva nkhaniyi ndipo adati aitanitsa mafumu onse a m’dera lake kuti awafunse nkhaniyo ndipo akatsimikiza aona momwe athanirane ndi mafumu omwe akukhudzidwa ndi mchitidwewu.

Mmalo ena monga Sonkhwe, Tsachiti, Kasemba ndi Kamphata kwa T/A Kalumbu, ogwira ntchito adadandaula kuti anthu sakufika mwaunyinji kukalembetsa chifukwa cha miyambo.

Pa Sonkhwe, anthu 1 698 ndiwo akuyembekezeka kulembetsa koma pofika Lolemba lapitalo, anthu 866 ndiwo adali atalembetsa ndipo woyang’anira pamalowo, Lemson Solomon, adati zinthu sizikuyenda chifukwa cha miyambo.

“Kukuoneka kuti ino ndi nyengo ya ziliza ndi maukwati koamnso chiyambireni kalembera, kwachitika maliro akuluakulu angapo zomwe zachititsa kuti anthu azitanganidwa mmidzi,” adatero Solomon.

Pamalo olembetsera a Tsachiti, anthu 2 120 akuyenera kulembetsa koma pofika lolemba, anthu 1 115 ndiwo adali atalembetsa ndipo woyang’anira malowo David Chikumba adati m’masiku 6 oyambirira, kudagwa maliro anayi m’midzi yozungulira.

Kupatula maliro, woyang’anira malo olembetsera a Kasemba, Laika Palikena, adati m’deralo mudali miyambo ya ufumu iwiri ndi ziliza zomwe zidatangwanitsa anthu.

“Poyamba kudali mwambo okwenza amfumu a Chimbalame ndipo pano mwambo olonga umfumu wa a Ndunga uli mkati. Kupatula apo kudali maliro atatu komanso ziliza ndiye zinthu sizikuyenda ayi,” adatero Palikena.

Mkulu wa bungwe la MEC Jane Ansah adati zopinga zokhudza miyambo n’zokulira bungwelo koma n’zongofunika kukambirana bwino ndi mafumu kuti

awone momwe angakonzere zinthu kuti kalembera asasokonekere.

“Miyambo ngati imeneyi komanso maliro ndi zinthu zomwe zimakhalako nthawi zonse chaka chonse kaya kuli kalembera kapena ayi ndiye n’zotikulira koma tiyesetsa kukambirana ndi mafumu,” adatero Ansah.

Ngakhale zili chonchi, bungwe la National Initiative for Civic Education (Nice) Trust lati akukhulupilira kuti akwanitsa chiwerengero cha anthu omwe akuyembekezera kulemba mgawoli.

Related Articles

Back to top button
Translate »