Mafumu alankhula pa chigamulo cha khoti pa CDF
Chigamulo cha khothi choletsa aphungu kuyendetsa ndalama zachitukuko za Constituency Development Fund (CDF) chapereka maganizo osiyana pakati pa anthu.
Khoti loona za malamulo (Constitutional Court) ku Lilongwe Lolemba lidagamula kuti thumba la CDF siloyenera kukhala m’manja mwa aphungu koma kuti pakhale munthu kapena komiti yapadera yoling’anira.

“Ntchito ya aphungu n’kupanga malamulo komanso kulondoloza momwe ndalama za boma zikuyendera,” lidatero khoti.
Mfumu yaikulu Mtwalo ya ku Mzimba inati chigamulocho chili bwino chifukwa aphungu ena amatenga ndalama za CDF ngati zawo ndipo akutukula dera ndi ndalama zawo.
“Ineyo ndili ndi umboni. Phungu wina adatiyankhapo kuti ‘iyitu ndi alawansi [mswahara] yanga’. Choncho chigamulo choti asiye kuyendetsa CDF n’chabwino kwambiri,” iwo anatero.
Mfumuyi inati aphungu ena amanamiza anthu kuti akuwapangira zitukuko n’cholinga choti adzawavoterenso pomwe ndalama zimachokera ku boma.
Koma mfumu yaikulu Chikumbu ya ku Mulanje inati ngati CDF ingaikidwe m’manja mwa mafumu, ndiye kuti dzina liyenera kusintha chifukwa lilipoli limaimira dera la phungu.
Koma iwo anati aphungu ayenera kupitiriza kutsogolera CDF chifukwa palibe umboni oti aphungu amalephera pa nkhani za chitukuko. Mfumuyi inati payenera kukhala komiti yomwe iziyang’anira momwe ndalamazi zikugwilira ntchito.
“CDF ikhalebe m’manja mwa aphungu, koma kuti pakhale makomiti amphamvu olondoloza ndalamazo,” atero a Chikumbu.
Nayo mfumu yaikulu Kalonga ya m’boma la Salima inati kusiyana kwa aphungu kukuchititsa kuti nthawi ina CDF iyendetsedwe bwino koma nthawi zina isokonekere.
“Aphungu ena amayendetsa bwino CDF ndipo ena amakaniza. Komabe ngati aphungu ambiri amachita bwino, akanawasiyira kuti apitirize,” inatero mfumu Salima.
Chigamulo cha khoti chidabwera malingana ndi pempho la bungwe la makhonsolo la Malawi Local Government Association (Malga) loti khothi litanthauzire ngati n’koyenera kuti aphungu azivota nawo ku makhonsolo.
Pa chigamulo chake, khoti linatinso aphungu sayenera kuyendetsa CDF yomwe ndi ya ndalama zokwana K2 million komanso K12 million yapadera ya chitukuko cha madzi.
Mkulu wa Malga a Hadrod Zeru Mkandawire ananyadira ndi chigamulocho. Iwo anati zithandiza kupititsa patsogolo ntchito yopereka mphamvu kwa anthu kudzera m’makhonsolo.
“Apapa zakhala bwino chifukwa aphungu ntchito yawo n’kupanga malamulo ndi kulondoloza ndalama zaboma, osati kuyang’anira zitukuko yomwe ndi ntchito ya anthu ena. Tizigawana ntchitozi,” iwo anatero.
Kadaulo pa ndale a Justin Dzodzi anati kukhala kovuta kuti anthu azindikire chifukwa anazolowera kuti ntchito za chitukuko zili m’manja mwa aphungu.
“Kupanga lamulo malingana ndi zomwe lachita khoti kusokoneza zinthu. Sikuti phungu ayenera kumatengapo gawo pa chitukuko, koma anthu ku dera amafuna phungu wachitukuko,” iwo anatero.



