Nkhani

Malawi wauma

Vuto la mafuta a galimoto lomwe lanyanya tsopano lakweza mkwiyo mwa Amalawi kaamba kakukwera kwa mtengo wa galimoto zonyamula anthu komanso zakweza nkhawa yoti izi zikhoza kusokoneza pulogalamu ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo ya AIP.

Malingana ndi a Malawi Energy Regulatory Authority (Mera) omwe amayang’anira za mafuta, vutoli lakula chifukwa dziko la Malawi lilibe ndalama za kunja zoitanitsira mafuta kuchoka kunja.

M’malo omwetsera mafuta mudali mizere ya itali

Mneneri wa Mera a Fitina Khonje adatsimikiza polankhula ndi Zodiak Broadcasting Station kuti makampani oyitanitsa mafuta akulephera kutero chifukwa akufunika ndalama zakunja kuti athe kugula mafuta kunjako n’kubweretsa kuno.

Nkhaniyi ikutha pafupifupi zaka ziwiri tsopano kuyambira pomwe a Mera, a National Oil Company of Malawi (Nocma) komanso makampani oitanitsa mafuta a galimoto kunja adayamba kusambira m’manja kusowa kwa ndalama zakunja.

Koma kadaulo wa za ulimi ku sukulu ya ukachenjede ya Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) a Christopher Mbukwa ati boma likapanda kusaka ndalama zakunjazo msanga, livutika kunyamula fetereza wa AIP.

“Vuto ilili ndi lofunika njira yokhazikika yothanirana nalo osati zomwe zikuchitikazi. Uno ndi October ndipo boma limayenera kuyambapo kunyamula fetereza wa AIP koma mmalo mwake mpomwe mafuta afika povutitsitsa,” atero a Mbukwa.

Mlembi wa unduna wa za malimidwe a Dickxie Kampani adati makampani 13 adasaina kale kuti agulitsa nawo fetereza wa AIP koma akudikira unduna wa za chuma, banki ya Reserve Bank of Malawi ndi mabanki ena kuti athandize ndi ndalama zakunja.

Iwo adati pali fetereza yemwe ali kumadoko amaiko ena ofunika kukatengedwa komanso fetereza wina ali kale m’dziko momwe muno ndipo boma liyamba kuutumiza m’misika yomwe alimi angakagulire.

“Fetereza apezeka, tikuyembekeza wina yemwe ali m’madoko akunja komanso kupatula apo, tili ndi fetereza wina m’dziko momwe muno yemwe tiyambire kugawa,” adatero a Kampani.

Koma a Mbukwa achenjeza kuti posachedwapa tikhala tikulowa mwezi wa November ndipo alimi amayenera kuti ayamba kale kugula fetereza kapena wafika kale m’misika kuti alimi azikhala n’chikhulupiriro.

“Apapatu zikusonyeza kuti ngati tifike November ndi December ndalama zakunja zisadaoneke ndiye kuti mafuta a galimoto akhalabe akuvuta ndipo izi zikhudza kwambiri pulogalamu ya AIP,” atero a Mbukwa.

Pozungulirazungulira m’mizinda ya Blantyre, Lilongwe, Zomba ndi Mzuzu, atolankhani athu adapeza kuti galimoto zambiri zimangoimikidwa mmalo ogulitsa mafuta kudikira mwachiyembekezo kuti mafuta akhoza kufika.

Anthu ena adauza atolankhaniwo kuti ntchito zawo zaima chifukwa akutaya nthawi n’kudikilira mafuta komanso ena adati zikawavutitsitsa akugona mmalo ogulitsa mafutawo.

Tidapezanso kuti eni galimoto ozingwa akukagula mafuta ku msika wa mbanda komwe akugula  lita imodzi pa mtengo wa K5 000 mmalo mwa K1 746 ndipo izi zachititsa kuti eni galimoto zonyamula anthu akweze mitengo.

Ena mwa eni galimoto zoterozo akutha masiku angapo asadapite ku msewu chifukwa chodikira mafuta kuti agule pa mtengo wovomerezeka ndi boma kuti mwina apangepo phindu.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button