Nkhani

Ulendo wotsiriza wa a John Tembo

Listen to this article

Thupi la mphangala pa ndale a John Tembo lidalowa m’manda Lachitatu ku mudzi kwawo kwa Kaphala kwa T/A Kachere ku Dedza pa mwambo womwe udakusira pamodzi a ndale, a mipingo, mafumu, ogwira ntchito m’boma ndi Amalawi ena.

Maliro awo adalandira sawatcha ya asilikali a nkhondo pa mwamba pa matamando ndi litaniya za mbiri yawo ngati munthu yemwe adatenga gawo lalikulu potukula ndale ndi chuma cha dziko la Malawi.

Mwambowo udayendetsedwa ndi asilikali ndipo adapatsa thupi la a Tembo ulemu woomba mfuti katatu mlengalenga komanso lipenga la ulemu losonyeza kuvomereza ntchito zawo m’dziko muno.

Mbendera ya boma yomwe adakuta nayo bokosi la malemu a Tembo idaperekedwa kwa mwana wawo John Tembo Junior kuti ikhale chikumbutso cha malemu bambo awo.

Mwambo wotsiriza woperekeza a Tembo udachitikira pa bwalo la masewero la Dedza komwe mbiri yawo idatamandidwa kenako nkunyamulidwa ndi asilikali a nkhondo ulendo wa ku nyumba yawo yomaliza.

Kudali misozi yosatha kuchoka kwa a ku banja ndi owakonda malemu a Tembo komanso nkhope zachisoni ndi zakugwa, zina zosakhulupirira kuti zidalidi ku mwambo wotsanzikana ndi tate pa ndale.

Koma mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera adapepesa anamalira ndi achisoni onse powauza kuti iyi idali nthawi yokondwelera moyo ndi ntchito za malemu a Tembo.

“Ngakhale ili nyengo ya chisoni, ndi nthawinso yoti tikumbukire zabwino zomwe adachitira dziko la Malawi ku ndale, chuma ndi chitukuko. A Tembo adali mmodzi mwa anthu omwe dziko la Malawi silingaiwale mwachangu,” adatero a Chakwera.

Iwo adapempha Amalawi kuti atengere mtima wa a Tembo wolimbikira pochita zinthu, kukonda anzawo komanso yemwe adagwira ntchito yotamandika pobweretsa umodzi m’dziko muno.

Pothirira ndemanga pa nkhaniyi pocheza ndi wailesi ya MBC ku mwambowo, mlongo wa a Tembo yemwe adapondana naye mayi Ivy Tembo adati malemu a Tembo adali munthu wokonda kumanga maubale ndi anthu.

“Kuyambira tili ana, a John Tembo amakonda kupanga maubale. Kulikonse komwe timapita ndi malemu abambo athu omwe adali abusa, a Tembo samachedwa kupeza anzawo,” adatero mayiwo.

Yemwe adali mkulu wachitetezo wa a John Tembo a William Phakamisa nawo adati moyo mwa John Tembo sudzachoka mumtima wawo chifukwa adali mlerankhungwa.

“Kupatula kutsogolera chitetezo cha a Tembo, nthawi zambiri ndimawayendetsa pa galimoto. Malemu a Tembo adali ndi masomphenya aakulu adziko lino komanso chipani cha MCP.

“Akhalako mndende pa zifukwa za ndale komanso ndimakumbukira ine kuti adagulitsako ina mwa minda yawo kuti athandize chipani cha MCP chitavutika thawi imeneyo chili kotsutsa,” adatero a Phakamisa.

Mlembi wachipani cha MCP a Eisenhower Mkaka adakhuza a Tembo ngati mtsuko wa upangiri pa ndale, pachuma, pakayedetsedwe ka dziko komanso chitukuko kotero imfa yawo idalanda dziko la Malawi kasupe wa zambiri.

Ena mwa anthu omwe adagwira ntchito ndi a Tembo monga a Nicholas Dausi omwe ndi mneneri wa chipani cha DPP, a Louis Chimango omwe adakhalako sipikala wa Nyumba ya Malamulo komanso a Brown Mpinganjira adatamanda moyo wa a Tembo. “A Tembo samasankha munthu ngakhale atasiyana zipani za ndale, adali munthu wokonda anzake,” adatero a Dausi.

Related Articles

Back to top button