Nkhani

Maphunziro alowa libolonje

Listen to this article
  • Mphunzitsimmodzi, ana 110
  • Komaaphunzitsi 10 000 akusowantchito

Dziko la Malawi lalephera kukwaniritsa loto lake loti pofika chaka chino, mphunzitsi mmodzi aziphunzitsa ana 60 okha. Lero, mphunzitsimmodziakuphunzitsaana 110, malinga ndi bungwe lomenyera ufulu pankhani zamaphunziro la Civil Society Education Coalition (Csec).

Izi zikuchitika pamene dziko lino lidapeza K126 biliyoni kuyambira 2010 kuchokeraku DFID, Global Partnership for Education (GPE), Arab Bank for International Development in Africa, Saudi Fund for Development   for International Development in Africa komansoOpec Fund for International Development (Ofid) zokwaniritsiralotoli. Zina mwandalamazo zidali ngongole pomwe zina zidalizongopatsidwa.

Chodabwitsa chake n’chotidziko lino lili ndi aphunzitsi pafupifupi 10 000 amene akungotambalala kusowa ntchito.

Mkulu wa Csec, Benedicto Kondowe wati dziko lino likufunikira aphunzitsi 36 000 kuti mphunzitsi mmodzi aziphunzitsa ana 60.

“Boma li kusowekera dongosolo chifukwa ndalama ndiye zikufika koma tikuvutikabe. Tikukambamu, mphunzitsi mmodzi akuphunzitsa ana 110 mwina 140,” adatero Kondowe.

“Tikusowekera aphunzitsi okwanira pamene ambiri akungokhala kusowa ntchito. Mituyathuikukoka?” adadabwa Kondowe.

Iye adati sakumvetsa chifukwa chimene boma likupitirizirabe kusula aphunzitsi pamene akamaliza maphunziro akusowa ntchito.

“Zomwe tidagwirizanandi a National Education Sector Plan zidalizoti mphunzitsi mmodzi aziphunzitsa ana 40, ndipo tidati izizitheke pofika 2018, komabe palibe chikuchitika,” adatero Kondowe.

Iye adati ngati mphunzitsi akuphunzitsa ana ambiri, zimasokoneza maphunziro chifukwa sangakwanitse kuwathandiza.

“Zimafunika kuti pena mphunzitsi athandize mwana pa yekha, apapa ndiye kuti mphunzitsi ali ndi ntchito yambiri yomwe sangakwanitse ndipo zikatere maphunziro amalowa pansi,” adatero Kondowe.

Koma mneneri mu unduna wa zamaphunziro Lindiwe Chide wati izi zachitika chifukwa cha akangaude atatu amene azinga unduna wake.

“Kuchulukana kwa anthu. Tili ndi ana ambiri kuposa amene tidawayerekeza zaka 10 zapitazo,” adatero Chide.  “Talepheranso kusula aphunzitsi ambiri kuchokera mu 2013 chifukwa cha ndalama—komanso talephera kuwalemba ntchito chifukwa cha khobiri.”

Iye watsutsa kuti mphunzitsi mmodzi akuphunzitsa ana 110.

“Ndibodza limenelo chifukwa padakalipano mphunzitsi mmodzi akuphunzitsa ana 77.”

Mlembi wa bungwe la mgwirizano wa aphunzitsi la Teachers Union of Malawi (TUM), Charles Kumchenga adati mpaka lero boma silidalembe aphunzitsi amene adawasula m’gulu la IPTE 10, IPTE 11, IPTE 12 ndi ODL.

“Tilibe chidwi ndi maphunziro, n’chifukwa chake tikungokamba nkhani imodzimodzi koma popanda chosintha,” adatero Kumchenga. “Kodi zitanthauzanji kumusula munthu koma palibe ntchito?”

Iye adati pa chaka, dziko lino limasula aphunzitsi pafupifupi 8 000 koma zimatenga zaka ziwiri kapena kuposa apo kuti boma liwapatse ntchito.

Boma silidaperekenso malipiro kwaaphunzitsi amene adamaliza maphunziro awo mu July 2016. Ophunzira amene sadafune kutchulidwa atero.

“Apapa ndiye kuti boma likuchulutsa ngongole zomwe akuyenera kupereka kwa aphunzitsi. Panopa ngongole yafika pa K1.7 biliyoni. Kodi adzabweza liti?” wadabwa Kumchenga.

Chide adati aphunzitsi amene adamaliza mu 2016 alandira ndalama zawo posachedwa.

Pa zomwe boma likuchita, iye adati boma silikugona pamene lakonza ndondomeko zatsopano kuti afikire ndondomeko zimene adakhazikitsa zochulutsa aphunzitsi.

“Boma likumanga sukulu zina zosulira aphunzitsi komanso sukulu zomwe zilipo kale zizidzadza kuti tikwaniritse ganizo loti mphunzitsi mmodzi aziphunzitsa ana 60,” adatero Chide pamene adalonjeza kuti posakhalitsa boma liyamba kulemba aphunzitsi onse amene lawasula.

Related Articles

Back to top button
Translate »