Nkhani

Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa

Listen to this article

Mtsutso wabuka ndi mmene mtsogoleri wa dziko lino, Lazarus McCarthy Chakwera, wasankhira nduna za boma lake.

Amalawi ena akuti sakuonapo cholakwika ndi mmene Chakwera wasankhira nduna zake chifukwa munthu amagwira ntchito ndi anthu omwe akuwakhulupirira, komanso omwe akumvetsetsa masomphenya.

Wasankha nduna 31: Chakwera

Koma Amalawi ena akuti ndi wokhumudwa chifukwa samayembekezera kuti mtsogoleriyu n’kumaninkha maudindo kwa anthu okhawo omwe adamuthandiza kugwetsa boma la Democratic Progressive Party (DPP).

Pokambirana pa masamba awo a mchezo mndandanda wa nduna utangotuluka kumene Lachitatu usiku, anthu ena amafunsana kuti zitheka bwanji banja limodzi kutulutsa nduna ziwiri.

“Abale mpaka bedi limodzi kumagonapo nduna ziwiri” adatero Margaret Banda pothirirapo ndemanga pa kusankhidwa kwa Mohammed Sidik Mia ngati nduna ya zamtengatenga ndi mkazi wake Abida Sidik Mia yemwe panopa ndi wachiwiri kwa nduna ya zamalo.

Nalo banja la mtsogoleri wakale wa dziko lino Dr Hastings Kamuzu Banda sadaliponye miyala kaamba koti asankhamo Khumbize Kandodo Chiponda kukhala nduna ya zaumoyo ndi mlongo wake Kenny Edward Kandodo yemwe watenga unduna wa za ntchito.

Nancy Tembo, mpongozi wa John Tembo, adamusankha kukhala nduna ya za nkhalango ndi zachilengedwe pamene Roy Akajuwe Kachale-Banda, mwana wa mtsogleri wakale wa dziko lino Joyce Banda, ndi nduna ya za malonda.

Koma Joseph Phiri wa ku Mdeka m’boma la Blantyre adati sakuonapo cholakwika ndi masankhidwe a ndunazi chifukwa mtsogoleri amagwira bwino ntchito ndi anthu omwe akuwakhulupirira, komanso omwe akudziwa masomphenya ake.

“Ngakhale ku America mwamuna ndi mkazi wake amatha kutumikira chipani chimodzi. Mwachitsanzo, Bill ndi Hilary Clinton ndi banja, koma akhala apatsidwa maudindo akuluakulu pa ndale.

“Kodi ndiye kuti mwamuna akapatsidwa udindo ndiye kuti mkazi sakuyeneranso kupatsidwanso udindo ngakhale ali ndi zomuyenereza?” adafunsa Phiri.

Mkuluyu akupempha Amalawi kuti apereke mwayi kwa ndunazi kuti zigwire ntchito zawo.

Wezi Moyo, mmodzi mwa anthu omwe amatsatira ndale m’dziko muno, watsutsa zomwe Phiri walankhula.

“Sindikuona chifukwa chosankhira banja lonse—mwamuna ndi mkazi wake— kukhala nduna,” adatero Moyo polankhula ndi Tamvani.

Amalawi ena akudabwa ndi kusankhidwa kwa Gospel Kazako, mwini wake wa wailesi ya Zodiak, kukhala nduna yofalitsa nkhani.

“Nduna yofalitsa nkhani imakhala m’gulu lounika m’mene mawailesi akugwirira ntchito, kodi wailesi ya a Kazako ikadzalakwira malamulo a dziko lino adzalola kuti itsekedwe?

“Apa zaonetseratu poyera kuti a Chakwera amasankha anthu omwe akuganiza kuti adathandiza kuti alowe m’boma osati omwe ali ndi luntha lotukula dziko lino.

Lachitatu Chakwera adasankha nduna 31 ndipo 12 mwa izo ndi amayi kuimirira 39 percent. Achiwiri kwa ndunazi ndi amayi okhaokha ndipo alipo 8.

Mwa ndunazi, 7 zimachokera ku Lilongwe komwenso Chakwera amachokera zomwe bungwe la Centre for Democracy and Economic Development Initiative (CDEDI) lati sizikuonetsa kusintha kulikonse pakati pa boma Tonse Alliance ndi DPP.

Danwood Chirwa, mmodzi wa akatswiri azamalamulo, adati ndi wokhumudwa ndi m’mene Chakwera wasankhira nduna za boma lake.

Iye adati Chakwera akadatengerapo phunziro pa Modecai Msisha yemwe adakana unduna kaamba koti samafuna anthu aziona ngati akumulipira chifukwa cha ntchito yotamandika yomwe adaigwira poimirira Chakwera ku khoti.

Msisha ndi yemwe amatsogolera gulu la maloya omwe amayimirira Chakwera pa mlandu womwe mtsogoleriyu amapempha khoti kuti likane kuti mtsogoleri wa DPP Peter Mutharika adapambana chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino cha pa May 21 2019 kaamba koti chidali ndi zolakwika zambiri.

Mtsogoleri wa dziko lino ndi mkulu wa apolisi ndi gulu la asilikari a nkhondo a dziko lino ndipo wachiwiri kwa nduna ya zachitetezo ndi Jean Sendeza.

Chakwera adasankha wachiwiri wake kukhala nduna yoona zokonza ndondomeko za chitukuko za boma, komanso kukonzanso magwiridwe ntchito a anthu a m’boma.

Lobin Lowe ndi nduna ya zamalimidwe ndipo wachiwiri wake ndi Agnes Nkusa Nkhoma, Felix Mlusu ndi nduna ya za chuma pamene Michael Usi amupatsa unduna wa nyama zakutchire ndi zokopa alendo.

Eisenhower Mkaka ndi nduna yoona za zakunja, Patricia Kaliati ndi nduna yoona za chitukuko ndi kusamalira anthu pamene Richard Chimwendo Banda ndi nduna yoona za chitetezo cha m’dziko.

Lingson Belekanyama ndi nduna ya maboma aang’onoang’ono ndipo wachiwiri wake ndi Halima Ali Daud; Titus Mvalo ndi nduna ya zachilungamo; Agnes Nyalonje ndi nduna ya maphunziro wachiwiri wake ndi Madalitso Kambauwa; Khumbize Chiponda ndi nduna ya za umoyo ndipo wachiwiri wake ndi Chrissie Kanyasho; Kandodo ndi nduna ya zantchito ndipo wachiwiri wake ndi Vera Kamtukule.

Newton Kambala ndi nduna ya za magetsi; Kezzie Msukwa ndi nduna ya za malo ndipo wachiwiri wake ndi Abida Mia.

Sosten Gwengwe ndi nduna ya zamalonda; Timothy Mtambo ndi nduna yophunzitsa anthu ndi kuluzanitsa anthu pamene Nancy Tembo ndi nduna ya zankhalango ndi chilengedwe. n

Related Articles

Back to top button
Translate »