Nkhani

Chakwera akwanitse malonjezo—HRDC

Listen to this article

Bungwe la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) lati maso ake akadali otsegula n’cholinga choti boma la Tonse Alliance lisaphwanye ufulu wa Amalawi.

Mkulu wa bungweli Gift Trapence wauza Tamvani kuti HRDC iwonetsetsa kuti mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wakwaniritsa zomwe adalonjeza Lolemba kuti achepetsa mphamvu zake.

Trapence: Maso adakali otsegula

Chakwera adapereka lonjezolo pamwambo wokondwerera kuti dziko la Malawi latha zaka 56 lili pa ufulu wodzilamulira.

Mtsogoleriyu adalonjezanso kuti azipita ku Nyumba ya Malamulo kukayankha mafunso okhudza momwe akuyendetsera dziko lino.

Chakwera adati awonetsetsanso kuti lamulo loti anthu akupeza mauthenga a boma mosavuta (Access to Information) layamba kugwira ntchito n’cholinga cholimbikitsa kuchita zinthu poyera, komanso kuchepetsa ziphuphu ndi katangale.

“Adalonjeza kuti achotsa mphamvu zina za Pulezidenti ndipo mphamvu zimenezi zikhudze ku nthambi ya zachitetezo. Pulezidenti akakhala ndi mphamvu zambiri, nthambi ya chitetezo imasanduka ngati yake osati ya dziko,” adatero Trapence.

Iye adapempha Chakwera kuti awonetsetse ku m’boma lake mulibe katangale ndi ziphuphu.

“Mphekesera za katangale zifufuzidwe ndipo mutu wake uzioneka,” iye adatero.

Related Articles

Back to top button
Translate »