Nkhani

Mchitidwe wogona ndi ana ukukula kwambiri

Pamene bwalo lina ku Zomba m’sabata yangothayi lidagamula kuti mphunzitsi wina ndi wosalakwa pa mlandu wogwiririra mwana wophunzira pasukulu ya Zobwe ku Chingale m’bomalo, bwalo la milandu m’boma la Phalombe lagamula bambo wina wa zaka 45 kukaseweza zaka 12 kundende pogona ndi mwana wa zaka 15.

Zigamulo ziwirizo zadza m’sabata imene apolisi alengeza kuti chiwerengero cha milandu yokhudza kugwiririra ana chidafika pa 1 045 pakati pa January ndi September chaka chino kuchoka pa 984 chaka chatha.

Apolisi atalengeza kukwera kwa milandu yokhudza kugona ndi ana, mmodzi mwa oyimira anthu pa milandu yemwenso ndi womenyera ufulu wa ana a Alexious Kamangira adati kugona ndi ana kumakula makamaka kaamba koutsanza mtima.

“Boma likuyenera kukhazikitsa njira zabwino zoteteza atsikana ku mchitidwewu komanso makolo ayenera kuteteza anawo. N’zachisoni kuti ambiri mwa atsikana amagwiriridwa ndi atate, malume, achimwene, asuweni ngakhalenso anzawo amene amayenera kuwateteza,” adatero a Kamangira.

Nkhani ya ku Zomba ikuti, bwalo la milandu la majisitiliti mumzindawo lidapeza Chisomo Francisco Gomani wosalakwa pa mlandu womuganizira kuti adagonana ndi mwana.

Malinga ndi zolembedwa pa tsamba la Facebook la nthambi ya boma yoimira oganiziridwa mwaulere ya Legal Aid Bureau, a Gomani adamangidwa ndi polisi ya Chingale pa 27 October 2023.

Kubwalo la milandu, woganiziridwawo adaukana mlanduwo ndipo mbali ya boma idabweretsa mboni zitatu: Mayi a mwanayu, mwanayo komanso kadaulo wa za chipatala.

M’muumboni wawo, mayi a mwanayo adauza bwalolo mchemwali wawo adabwera mkati mwa usiku kudzawauza kuti adaona amuna awo ali matimati ndi mwanayo m’nyumba ina. Mayiwo adaonjeza kuti atapita kunyumbayo adawapezadi awiriwo, koma mwanayo adathawa.

Iwo adati pamalopo adapezapo kondomu imene idali ndi magazi.

Ndipo mu umboni wawo, wachipatala Catherine Maganizo adati atamuyeza mwanayo adapeza kuti adagonanapo ndi mwamuna kangapo konse.

“Ku mbali yake, mwanayo adauza bwalo kuti adapita kunyumba kwa a Gomani limodzi ndi mnzake kuti akathandize kuchonga mayeso, koma sadanene kalikonse kokhudza nkhani imene apolisi adawaitanira kuti akachitire umboni,” chidatero chikalatacho.

Umboni utaperekedwa, woimira a Gomani kuchokera ku LAB a Hanleck Ching’anda adatsindika kuti woganiziridwayo alibe mlandu woti ayankhe chifukwa umboni womwe bwalo lidapatsidwa siudali wogwira mtima. Iwo adapitirizanso kuti mayi a mwanayu adabwera ndi umboni omwe unali mphekesera chifukwa kondomu imene adatchulayo sadabwere nayo komanso mwanayo sadauze bwalo kuti nkhaniyo ndi yoona.

M’chigamulo chake, a majisitilitiwa a Martin Chipofya adagwirizana ndi LAB kuti a mbali ya boma sanabwere ndi umboni wokwanira wotsimikiza kuti Gomani anagonana ndi mwana.

Bwalolo lidaonanso kuti umboni unali wosakwanira komanso wosadalilika kuti mpaka munthu amangidwe. Kotero bwalo lidapeza mphunzitsiyo kuti alibe mlandu woti ayankhe malingana ndi zomwe amaganiziridwa.

Izi zili apo, bwalo la milandu ku Phalombe lagamula a Alfred Kamoto wa zaka 45 kuti akaseweze zaka 12 atapezeka wolakwa pogona ndi mwana wa zaka 15.

Mneneri wa polisi ya bomalo a Jimmy Kapanja adati bamboyo wakhala akugona ndi mwanayo pakati pa November ndi mwezi uno ndipo izi zidaululika pomwe mkuluyo ankanena kuti mwanayo wamubera ufa.

A Kapanja adati: “Mayi a mwanayo atafunsa chifukwa chimene adabera ufa, mwanayo adaulula kuti Kamoto adalephera kukwaniritsa zimene adalonjeza. M’bwalo la milandu mkuluyo adauvomera mlanduwo ndipo adapempha woweruza kuti apereke chilango chocheperako chifukwa ndi mutu wa banja lake.”

Iwo adaonjeza kuti oyimira boma adati woweruza asamvere izi chifukwa kugona ndi mwana ndi mlandu waukulu ndipo a Leonard Mtosa adapereka chilangocho kwa bamboyo.

Malinga ndi mkulu wa bungwe loona zaufulu wa ana la Yoneco a MacBain Mkandawire adati kupyolera m’njira yoimba mafoni ya Tithandizane Helpline amalandira nkhani 5 kapena 6 pa tsiku za ana amene agonedwa.

“Awa ndi ana amene amapereka malipoti awo. Nanga amene nkhani zawo zimangothera mumtima? Pakuyenera kukhala njira zotetezera anawa,” adatero a Mkandawire.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button