Ming’alu m’kalembera wa chisankho cha 2019

Pamene kalembera wa chisankho cha pa 21 May 2019 akuyamba Lachiwiri likudzali, akadaulo ena awona kale ming’alu yakudza chifukwa chokana bilo yoyendetsera malamulo a zisankho ku Nyumba ya Malamulo.

Mwa zina, malamulowo akadasinthidwa, Gawo 77 la malamulo aakulu a dziko lino—Constitution—likadasinthidwa kuti lifanane ndi Ndime 15 la malamulo oyendetsera zisankho. Pakadalipano, malamulo awiriwo amakhulana pomwe lamulo la zisankho limati olembetsa akhale amene adzakhale atakwanitsa zaka 18 tsiku lovota pomwe Gawo 77 limati olembetsa akhale okwana zaka 18 tsiku lolembetsa.

Nkhani ina yayala nthenje ndi zitupa zolembetsera pamene bungwe loyendetsa zisankho likuti Amalawi ayenera kudzagwiritsa ntchito chitupa cha unzika polembetsa pomwe malamulo a chisankho amati zitupa zololedwa pa kalemberayo ndi pasipoti, chitupa choyendetsera galimoto ndi zina zotero.

Aphungu adali ndi mpata wosintha malamulo oyendetsera zisankho pamsonkhano wawo mu December chaka chatha koma zidakanika.

MEC yatsindika kuti polemba anthu m’kaundulayu lidzalola kulemba ngakhale omwe sadakwane zaka 18 koma pali umboni woti zakazi zidzakwana pofika tsiku lotseka kalembera.

“Lamulo limalola yemwe wafika zaka 18 zakubadwa kulowa m’kaundula ndipo tipereka mpata olembetsa kwa omwe adzakwanitse zaka 18 pofika tsiku lotseka kalembera pa 9 November 2018,” latero bungwe la MEC.

Izi zikusemphana ndi momwe zimayendera pazisankho za mmbuyomu pomwe bungweli limapereka mpata kwa omwe adzakwanitse zaka 18 pofika tsiku lovota kulowa nawo m’kaundula.

Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe oona za zisankho la Malawi Electoral Support Network (Mesn), Steve Duwa, wati ngakhale palibe mlandu ulionse omwe bungwe la MEC likupalamula, ufulu wa anthu omwe adzakwanitse zaka 18 pofika tsiku lovota ukuphwanyidwa.

Duwa wati izi zili chomwechi chifukwa pali malamulo awiri osiyana okhudza nkhani ya zaka zokavotera.

Kadaulo wa zamalamulo kusukulu yaukachenjede ya Chancellor College Edge Kanyongolo wati malamulowa ndi awiri lina ndi ndime chabe pomwe lina ngati lomwe lasankha kugwiritsa ntchito bungwe la MEC ndilo lamulo lalikulu ladziko la Malawi.

Ndime yachisanu (5) komanso 199 za lamulo lalikulu la dziko la Malawi zimati pomwe gawo lililonse la malamulo likusemphana ndi lamulo lalikulu la dziko, lamulo lalikululo ndilo lidzagwire ntchito osati gawo chabelo.

“Kutengera malamulo, panopa mpomwe bungwe la MEC latsatira zoyenera kutsata chifukwa likugwiritsa ntchito zomwe lamulo lalikulu limanena kusiya zomwe gawo chabe limanena,” adatero Kanyongolo.

Iye adati ngakhale watero, mpovuta kugamula kuti m’zisankho za mmbuyomu, MEC imasokoneza kayendetsedwe ka zisankho chifukwa padalibe yemwe adabwera poyera kudzadandaula pa  momwe bungwelo limasankhira lamulo lotsatira.

Bungwe la MEC lati latsata njirayi pofuna kupewa chinyengo cha mtundu uliwonse komanso pofuna kuti ntchitoyi idzayende mwachangu pogwiritsa ntchito makina apamwamba a kompiyuta pochita kalemberayu.

“Chomwe tikufunira chitupachi n’choti munthu ngati walembetsa kale kulikonse, ngakhale atasintha kokavotera, kompyuta idzadziwa kuti walowa kale m’kaundula choncho palibe kupusitsa MEC ndipo zipani zonse zofuna chilungamo zikuyenera kukondwa ndi njirayi.

“Kupatula apo, tsiku lodzavota, munthu yemwe wavota kale, kompyuta izidzamukana kuvotanso ndipo kudzakhala kosavuta kudziwa kuti anthu omwe avota ndi angati. Palibe mpata obera apapa,” adatero wapampando wa komiti yoyang’anira zofalitsa nkhani ndikuphunzitsa anthu ku MEC, Commissioner Moffat Banda.

Iye wati pali ndondomeko yoti aliyense yemwe akuyenera kulowa m’kaundula ndipo ali ndi khumbo lotero adzathandizidwe mpaka adzalowe m’kaundula.

“Pamalo olembetsera aliwonse pazidzakhala a nthambi ya kalembera wa unzika ya National Registration Bureau (NRB) yomwe izidzatithandiza kulemba omwe sadalembetse kapena omwe adataya chitupa chawo,” adatero Banda.

Iye adati kwa omwe alibe chitupa cha unzika chifukwa sichidatuluke, chidasowa kapena adali asadalembetse, azidzadzera m’manja mwa NRB yomwe izidzawapatsa tikiti yomwe ili ndi zomwe MEC ikufuna m’zitupa.

Mkulu woyang’anira za maubale ku mgwirizano wa maiko a ku Ulaya, Lluis Navarro, adapempha kuti pakufunika kuchilimika pankhani yophunzitsa anthu zachisankho chikudzachi ndi kuwamema kuti akalembetse.

Share This Post