Nkhani

Mipingo yadzudzula nkhanza

Listen to this article

Atsogoleri a mipingo ati nkhanza makamaka zochitira ana ndi amayi zanyanya m’dziko muno moti asungwana 21 pa 100 aliwonse komanso anyamata 14 pa 100 aliwonse amagwiriridwa ku umwana wawo.

Atsogoleriwa omwe ali pansi pa bungwe la atsogoleri a zipembedzo la Public Affairs Committee (PAC) atulutsa chikalata chomwe chikufotokoza kuti dziko la Malawi silikupanga bwino pa nkhani yoteteza ana.

“M’dziko lonse, Malawi ili pa nambala 7 pa mndandanda wa maiko omwe akukwatitsa ana achichepere. Pafupifupi theka la asungwana amalowa m’banja asadafike zaka 18 ndipo 33 pa 100 aliwonse amakhala atabereka kale pokwana zaka 18,” chatero chikalatachi.

Atsogoleriwa adalemba kalatayi atakambirana kwa masiku 5 pomwe amalandira upangiri wa katetezedwe ka ana kuchokera ku bungwe loona za ana la Unicef kuyambira Lolemba mpaka Lachisanu sabata yatha ku Mponela m’boma la Dowa.

Atasainira kalatayo, mkulu wa bungwe la PAC Rev Felix Chingota adati n’zomvetsa chisoni kuti nkhanza zotere zikuchitika pomwe dziko la Malawi lidasayinira pangano loteteza ana mumgwirizano wa maiko onse wa United Nations (UN).

Pazokambiranazo, atsogoleriwo adakambiranapo za kugwiriridwa kwa atsikana m’zitokosi zapolisi komanso kugwiriridwa kwa ana asukulu ku Karonga ndi amayi kwa Msundwe m’boma la Lilongwe.

Atsogoleriwo adadzudzulanso atsogoleri ena a mipingo omwe amakhudzidwa ndi nkhanza zochitira ana komanso adindo ena omwe amapalana ubwenzi ndi ana kapena kuwagwiririra.

Kupatula kusayinira pangano la maiko, dziko la Malawi lili ndi malamulo komanso mfundo zolimbikitsa kuteteza ana ndi kuthetsa nkhanza monga lamulo loti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo, lamulo loteteza, kusamalira ndi kupereka chilungamo kwa ana, kuthetsa nkhanza za m’banja komanso ndondomeko yoletsa maukwati a ana.

Wachiwiri kwa mkulu wa bungwe la Unicef ku Malawi Margarita Tileva adati Malawi ali ndi malamulo komanso ndondomeko zabwino ndipo adati izi zingathandize ngati ndondomekozi ndi malamulowa zingagwire ntchito moyenera.

“Ndasangalala ndi zokambiranazi makamaka zomwe apanga atsogoleri a mipingo kulemba kalatayi yomwe siyikupsatira momwe nkhanza zilili m’dziko muno moti ndikupempha kuti chonde tiyeni tigwiritse ntchito malamulo ndi ndondomeko zomwe tilinazo,” adatero Tileva.

Mkulu wazofalitsa nkhani ku unduna wa zofalitsa nkhani Grace Kwalapu yemwe amayang’aniraso za zosindikiza mauthenga watsimikiza kuti ana makamaka asungwana komanso amayi akuchitidwa nkhanza ndipo wati boma liwonjezera moto ophunzitsa anthu za Malamulo kuti nkhanzazo zithe.

Related Articles

Back to top button