Mkonono wanyanya kotsutsa
Akadaulo pa nkhani zosiyanasiyana m’dziko muno ati mbali yotsutsa boma ili ndi benthu lake pa mavuto omwe Amalawi akudutsamo chifukwa mbaliyo yalephera kugwira ntchito yake moyenera.
Malingana ndi kadaulo pa ndale a Ernest Thindwa, udindo wa otsutsa boma n’kuunikira pomwe boma likulephera ndi kupereka maganizo awo pa momwe zinthu zikuyenera kuyendera kuonetsa momwe iwo angakonzere zinthu atalowa m’boma.
Koma a Thindwa ati otsutsa a lero akukhala ngati ali mtulo kapena akukhalira dala chete kuti adzapeze chonena nthawi yokopa anthu ya kampeni ikadzafika pomwe akuyembekeza kudzagwiritsa ntchito kufooka kwa anzawo.
“Otsutsatu ndi boma la chiyembekezo ndiye zimafunika kuonetsa chiyembekezocho pomwe mukutsutsa osati kudikira za agwetsa ntola ayi. Anthu akaona momwe mukuperekera mfundo ku boma la nthawi imeneyo mpomwe amakhala nanu n’chiyembekezo,” atero a Thindwa.
Pomwe kadaulo pa za chuma a Christopher Mbukwa omwe amaphunzitsa kusukulu ya ukachenjede ya Mzuzu University ati mbali yotsutsa ya ulendo uno ikungokhala ngati ili mbali ya boma chifukwa ikulekerera chilichonse chabwino ndi choipa chomwe.
Iwo ati mwachitsanzo poona momwe ndondomeko ya zipangizo zaulimi zotsika mtengo ya AIP ikulephera, otsutsa amayenera kukwera pachulu kulimbana ndi boma kuti pulogalamuyo isinthidwe koma nawo angotsatira mmbuyo.
“Vuto lakula ndi ndale, aliyense amatenga ngati pulogalamu ya AIP ndiyo chopambanira zisankho ndiye ngakhale ikulephera kuonetsa zipatso zoyenera, otsutsa sakulankhulapo kanthu moti kuti ipite ku Nyumba ya Malamulo akayisapotanso,” atero a Mbukwa.
Iwo ati otsutsa amayenera kukhala pansi ndi kusanthula vuto lililonse palokha n’kupeza mayankho ake ndi momwe mavutowo angathere n’kubweretsa m’Nyumba ya Malamulo kuti boma litolemo zomwe likuona kuti n’zothandiza.
Dziko la Malawi likudutsa m’nyengo zovuta zomwe zambiri sizikuyenda monga kukwera kwa mitengo ya katundu, kusowa kwa mafuta komanso kugawa kwa ndalama ya Kwacha ndi kusowa kwa ndalama za kunja komwe kukupangitsa kuti boma ndi makampani azilephera kuitanitsa katundu kunja.
Koma omenyera ufulu anthu ogula katundu a John Kapito ati izi zikuchitika chifukwa utsogoleri ku mbali yotsutsa boma sukuoneka ndiye boma nalo likupanga zinthu pozindikira kuti palibe olitsutsa kapena kulidzudzula.
Iwo ati mwachitsanzo, momwe njala yayambira kuvutamu, otsutsa amayenera kuitana boma kuti aonere limodzi zoyenera kuchita koma mmalo mwake angotaya nthawi nkulankhula kenako nkukhalanso chete osawonetsa khumbo lenileni lofuna kuthana ndi vuto lomwe lilipo.
“Kukuwuzani zowona, pomwe zafikapa zikuwoneka kuti otsutsa akungodikira milakuli yoti mwina nkupeza mpata wolowa m’boma koma kutengera kusoweka kwa utsogoleri komwe kulipo mbali yotsutsa, maloto amenewo ndi a chumba,” atero a Kapito.
Iwo ati mpata wa otsutsa wodzigulitsa ngati boma la chiyembekezo ndi omwe ukutsukuluzika n’kukhala chete kwaona ndipo wachenjeza kuti akapitiriza momwe akuchitira, adzavutika kudzigulitsa kwake.
Pa maliro a a John Tembo sabata yatha, mmodzi mwa amkhalakale pa ndale a Brown Mpinganjira adayamikira kuti panthawi yawo ya a Tembo, mbali yotsutsa idali yamphamvu ndipo idathandiza boma la nthawiyo la a Bingu Wa Mutharika liyende bwino.
A Mpinganjira adati chifukwa cha kuchilimika kwa mbali yotsutsa nthawiyo, boma silimapanga zobwerera mmbuyo mpaka Amalawi adayamikira ulamuliro wa a Bingu Wa Mutharika wa teremu yawo yoyamba chifukwa cha momwe otsutsa amagwirira ntchito yawo.
Koma mtsogoleri wa mbali yotsutsa boma a Kondwani Nankhumwa imangosonyeza kuti akulankhulapo mmene tilili kuyesa kuti timve maganizo awo pa zomwe akadaulowo adanena.
Koma magulu osiyanasiyana akhala akudzudzula mbali yotsutsa boma makamaka chipani cha Democratic Progressive (DPP) chomwe nchachikulu kotsutsako kuti chikutaya nthawi ndi mikangano ya mkatikati mwa chipani.