Nkhani

Unicef ilipilira asungwana 5 600 fizi

Listen to this article

Asungwana 5 600 omwe akadalephera sukulu kaamba ka vuto la fizi achita mwayi ndi lonjezo la bungwe la United Nations Children’s Fund (Unicef) kuti lipereka ndalama zothandizira asungwana kwa zaka 5.

Pokumbukira tsiku la asungwana chaka chino, bungwe la Unicef lidatulutsa kalata yolonjeza kuti lipereka thandizolo kudzera ku bungwe la Campaign for Female Education (Camfed) kuti lilimbikitse asungwana kupita patali ndi sukulu.

Bungwe la Unicef lati limazindikira kuti asungwana ambiri sapita patali ndi maphunziro ndipo ambiri amakathera m’mabanja akadali aang’ono chifukwa sapatsidwa mpata ofanana ndi anyamata.

“M’Malawi muno, asungwana 42 mwa asungwana 100 alionse amakwatiwa asadafike zaka 18 ndipo 9 mwa asungwanawo amakwatiwa asadakwane zaka 15. Fizi yomwe tipereke ndi kukwaniritsa lonjezo lathu lotukula maphunziro aasungwana,” yatero kalata ya Unicef.

Mwambo wachaka chino udakumbukiridwa pa mutu woti, ‘Liwu langa, tsogolo la tonse’ ndipo nduna yoona zoti pasamakhale kusiyana pakati pa amuna ndi amayi, ana ndi chitukuko cha mmadera mayi Jean Sendeza adati mutuwo ukugwirizana kwathunthu ndi masomphenya a Malawi 2063.

“Masomphenya adziko la Malawi amayika patsogolo mawu woti osasiya aliyense mmbuyo kotero mpofunika kwambiri kuti pomwe tikupanga mapulogalamu, tisamayiwale asungwana monga momwe mutu wamwambo ukunenera,” adatero a Sendeza.

Iwo adati ngakhale pali mapulogalamu ndi ndondomeko zofuna kutukula asungwana, iwo akukumanabe ndi zowabwezera mmbuyo zosiyanasiyana zofunika mabungwe agwire ntchito limodzi ndi boma kuti zipsinjozo zigonje.

“Monga mukudziwa kuti boma lidapanga malamulo ndi ndondomeko sotetezera asungwana komanso apulezidenti a Lazarus Chakwera adasayina mapangano osiyanasiyana ndi mayiko ena ndi udindo wathu kuwonetsetsa kuti zimenezi zikugwira ntchito,” adatero a Sendeza.

Posachedwapa, mneneri wa unduna wazamaphunziro a Mphatso Nkuwonera adati undunawo udakhazikitsa pulogalamu yomwe kudzera mmabungwe uzigwira ntchito ndi asungwana omwe amaliza maphunziro asekondale kuti azilimbikitsa asungwana anzawo.

“Tikufuna kuti asungwanawo aziyendera anzawo n’kumawafotokozera momwe iwo adakwanitsira kumaliza maphunziro ngakhale amadutsa muzopinga kuti enawo azitolako nzeru,” adatero a Nkuwonera.

Mkulu wa bungwe lolimbikitsa ufulu wa asungwana la Malawi Girl Guides Association (Magga) mayi Mphatso Jimu adayamikira ganizolo ponena kuti asungwana ambiri sapita patali chifukwa chosowa chilimbikitso.

Related Articles

Back to top button