Nkhani

Mkulu wa kunyumba ya chisoni agwidwa ndi ziwalo

Listen to this article

Abambo awiri omwe amagwira ntchito kunyumba yachisoni kuchipatala cha Kamuzu Central (KCH) akuzengedwa mlandu wodula maliseche a mtembo wa munthu wamwamuna omwe unali m’nyumbayo poyembekezera kuti abale ake adzautenge.

Mneneri wa polisi ya Lilongwe, Ramsy Mushani, watsimikiza za nkhaniyi ponena kuti aganiziridwawa, Lufeyo Mphimbi, wa zaka 54, ndi Samalani Jabu, wa zaka 58, adadula ziwalozo anthu ena atawauza kuti pali msika wa K8 miliyoni wa ziwalo za munthu wamwamuna.

Mushani wati anthu omwe akuwaganizira kuti adapeza msikawo, Sebita Mwale, wa zaka 27, ndi Eric Mwandira, wa zaka 34, adalonjeza ogwira ntchito kunyumba yachisoniwo kuti malonda akatheka adzawapatsa theka la ndalamazo.

Mushani wati apolisi adagwira ndi kumanga Mwale ndi Mwandira pamalo omwetsera mafuta a galimoto a Kaunda pamsewu wopita ku Mchinji atatsinidwa khutu ndi anthu ena kuti awiriwo adali ndi maliseche a munthu wamwamuna omwe amagulitsa.

“Atafunsidwa za ziwalozo iwo adaulula kuti adachita kupatsidwa ndi abambo Awiri, Mphimbi ndi Jabu, omwe amagwira ntchito kunyumba yachisoni ku KCH ndipo onse anayiwa adavomera kuti adatenga nawo gawo pankhaniyi,” adatero Mushani.

Iye adati Mwandira adapita kunyumba ya chisoniyo kukakumana ndi Mphimbi, yemwe ndi mnzake wakalekale, kukakambirana za nkhaniyo ndipo anthuwo adakambiranadi muofesi ya Jabu n’kumvana.

“Atagwirizana za malipiro Mphimbi ndi Jabu adalowa m’chipinda chosungiramo mitembo momwe adatulukamo ndi malisechewo n’kuwapereka kwa Mwandira yemwe adatengana ndi Mwale kuti akagulitse koma anthu adatsina khutu apolisi msanga,” adatero Mushani.

Mwale ndi Mwandira akuwazenga mlandu wopezeka ndi ziwalo za munthu, zomwe zitsutsana ndi ndime 16 yokhudzana ndi thupi la munthu m’malamulo a dziko lino, pomwe Mphimbi ndi Jabu akuyankha mlandu wodula ziwalo za munthu wakufa kutsutsana ndi ndime 18 ndinso wopereka ziwalozo kuti zitsatsidwe malonda kutsutsana ndi ndime 16 (gawo B) la malamulo okhudza za thupi la munthu.

Bwalo la milandu ku Lilongwe Lachiwiri lapitali lidakana kutulutsa anthu anayiwa pabelo chifukwa ati likuopa kuti akhoza kuthawa.

Pogamula pempho la owayimira anayiwo pamlanduwo, Alemekezeke Mando ndi Chris Tukula, kuti apatsidwe belo, woweluza milandu kubwaloli magisitiriti Patrick Chirwa adati kupatsa belo anthuwo n’kovuta chifukwa mlandu wawowo ndi woopsa.

“Ndili ndi mantha kwambiri paganizo lopatsa anthuwa belo chifukwa pali chiopsezo chakuti chilungamo chikhoza kusokonezeka komanso chikhulupiriro chomwe anthu ali nacho mubwalo lino chikhoza kuonongeka,” adatero Chirwa.

Mkulu wa chipatala cha KCH, Noordeen Alide, samapezeka pafoni yake yam’manja kuti alankhuleko pankhaniyi makamaka mmene ntchito ya kunyumba yachisoniyo imayendera.

Mphimbi amachokera m’mudzi mwa Chipazi, T/A Msakambewa, ku Dowa ndipo Jabu amachokera m’mudzi mwa Msimbi, T/A Masula, ku Lilongwe. Mwale kwawo ndi kwa Chipoza, T/A Santhe, ku Kasungu, pomwe Mwandira

ngwa ku Mwazisi, kwa Themba la Mathemba Chikulamayembe ku Rumphi.

Related Articles

Back to top button
Translate »