Nkhani

Woba chiponde ku Chiladzulu agwidwa

Listen to this article

Bwalo la Chiradzulu layamba kuzenga mlandu Operations Manager wa kampane yolondera ya Global Communications Centre pomuganizira mlandu woba chiponde cha odwala a pachipata cha bomalo.

Mneneri wapolisi ya Chiradzulu, Ralph Makondetsa watsimikizira zakunjatidwa kwa Blessings Yonamu wa zaka 29 yemwe ndi wa m’mudzi mwa Mwabwila kwa T/A Malili ku Lilongwe.

Makondetsa wati akuganizira mkuluyu kuti pa 9 May adalowa m’siling’I ya nyumba yomwe mumasungidwa chipondecho.

M’menemo akuti adaba makatoni 9 a chipondecho. M’katoni iliyonse mumakhala timapakete 250 kusonyeza kuti m’makatoni onsewa mudali mapakete 2250.

“Titatsinidwa khutu tidayamba kusaka mkuluyu ndipo tidamujata. Mlandu udalowa Lachiwiri lathali koma iye wakana. Pa 29 mlanduwu upitirira,” adatero Makondetsa.

Ntchito zina ndi chiletso

Anthu ena ndi akhama mpaka chomwe akufuna chitatheka. Chithunzi tikuwonacho ndi ntchito ina yomwe tidayiwona m’boma la Ntcheu. Pamenepa anthuwo akukweza ng’ombe m’galimoto. Ng’ombezo azigula ndiye akufuna ziyende m’galimotoyo.

Ng’ombezo zidalipo zinayi, pamalopa padali matatalazi chifukwa pena yokwerakwera imapezeka kuti yapulumuka ndi kuthawa. Zina zimagunda pomwe akukweza. Aliyense apa amakhala wochenjera kuwopa kuti ingamusenze.

Related Articles

Back to top button
Translate »