MLS yalasa!

Bungwe la akadaulo a za malamulo m’dziko muno la Malawi Law Society (MLS) ladzudzula zipani za ndale, mkulu wa bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC), apolisi komanso okonza zionetsero pa mkokemkoke umene wabuka kutsatira zolengeza za chisankho cha pa 21 May.

Bungwe la MEC motsogozedwa ndi Jane Ansah lidatulutsa zotsatira za chisankho pomwe lidati mtsogoleri wa chipani cha DPP Peter Mutharika ndiye adapambana chisankhocho motsatizana ndi Lazarus Chakwera wa MCP pomwe Saulos Chilima wa UTM adali wa chitatu. Koma Chakwera ndi Chilima adatengera kukhoti MEC ndi DPP ponena kuti chisankhocho sichidayende bwino.

Ansah: Ndiwayankha a MLS

Pambuyo pa izi, mgwirizano wa mabungwe omenyera ufulu wa anthu wa Human Rights Defenders Coalition (HRDC) wakhala ukukonza zionetsero zofuna kuti Ansah atule pansi udindo. Pazionetserozo pakhala pakuchitika zipolowe ndipo katundu wina wa boma komanso wa anthu ena wakhala akuonongedwa.

Lachitatu MLS idalembera kalata Mutharika, Chakwera, Chilima, Ansah, mkulu wa HRDC Timothy Mtambo, sipikala wa Nyumba ya Malamulo Catherine Gotani Hara komanso mkulu wa apolisi Rodney Jose, kutambasula zolakwika zimene iwo akuona.

Chikalatacho adasayinira ndi mlembi wa MLS Martha Kaukonde ndipo chidati chikudabwa kuti ngakhale pali ziwawa zoti Ansah achoke, iye sakuchoka. “Katundu akuonongeka wochuluka. Bwanji osangotula pansi udindowo?” idatero kalatayo.

MLS idadzudzula atsogoleri a ndalewo ati chifukwa sakuuza bwino owatsatira kuti mlandu umene uli kukhoti ukhonza kukomera aliyense. “Tikudabwa kuti andalewo akuchititsa misonkhano ngati ndi nthawi ya kampeni mmalo mowakonzekeretsa owatsatira kuti khoti likhoza kugamula mosawakomera malingana ndi zonenedwa mukhoti. Tikumbutsane kuti ndi MEC komanso bwalo la milandu lokha limene linganene ngati chisankho chidayenda bwino kapena ayi. Zopereka maumboni pa mchezo wa Internet sizitithandiza,” idatero kalatayo.

Kalatayo idadzudzulanso Mutharika kaamba kolola otsatira chipani chake kuchita zionetsero za mpikisano motsutsana ndi amene akuti sadapambane. Sabata yatha, otsatira chipani cha DPP adayenda mumzinda wa Blantyre ndipo adakathera kunyumba ya Sanjika kumene Mutharika adawatsimikizira kuti chipani chake chipitiriza kulamula mpaka 2084.

Iyo idati HRDC iyenera kulingalira mozama za zionetsero zimene yakhala ikukonza ngati zingapindulire mtundu wa Amalawi.

MLS idadzudzula apolisi polephera ntchito yawo yoteteza Amalawi ndi katundu wawo nthawi ya zionetserozo. Pamene ofuna kuti Ansah achoke adachita zionetsero, otsatira ena adamenya anthuwo ndipo apolisi amangoyang’ana. Asirikali a Malawi Defence Force (MDF) ndiwo adaletsetsa anthuwo.

“Chofunika tsopano n’choti pakhale kukambirana pakati pa onse okhudzidwa kuti bata ndi mtendere zibwerere m’dziko muno,” idatero kalatayo.

Pempho loti pakhale kukambirana likudza pomwenso bungwe la mipingo loona momwe zinthu zikuyendera m’dziko muno la Public Affairs Committee (PAC) lakumana kale ndi Chakwera komanso Chilima amene avomereza kukambiranako. Wapampando wa bungwelo Ambuye Thomas Msusa ndiye akuyenera kuluzanitsa atatuwo ndipo akuyenera kukumana kaye ndi Mutharika kuti akonze tsiku la zokambiranazo.

Polankhula ndi mtolankhani wathu, Chakwera adati adalandira kalatayo koma amayembekezera kumva kuchokera kwa alangizi ake pa za malamulo asanayankhepo kanthu. Chilima naye adati adalandira kalatayo koma adati mneneri wa chipani chake Joseph Chidanti-Malunga ndiye angayankhe. Koma Malunga adati sanakambirane zoti anene.

Ansah adati ayankha a MLS pa zomwe adalembazo.

Mlandu wa chisankho ulowanso m’bwalo Lachisanu likubwerali mumzinda wa Lilongwe. MLS ikutenga nawo mbali pamlanduwo pounikira bwalolo zina ndi zina zokhudza malamulo.

Share This Post