Nkhani

 Mneneri akhala osadya komanso kumwa masiku 40

 Mneneri Ellason Zande akuti anafa n’kudzukanso pomwe anasala kudya kwa masiku 40, Mulungu atawaonekera.

A Zande omwe akuchita utumiki wawo m’boma la Chiradzulu pampingo wa Nazarete Prophetic Church of All the Nations ati anatumidwa asanabadwe chifukwa mayi wawo anawauza kuti ngakhale ali mwana, bambo awo amakana kuti simwana wawo chifukwa amachita zinthu zodabwitsa.

Akuti Yesu wakhala akuwaonekera: A Zande

Mpingowu uli msewu wa Midima, pa Losa.

A Zande omwe anabadwa chaka cha 1965 akuti Yesu anayamba kuwaonekera ali mwana ndipo anakhala akumuuza wa nsembe, panthawiyo n’kuti ali a mpingo wa Katolika.

“Ndikamuuza wa nsembeyu, ankandiyankha kuti akumaona nyali yanga ikuwala kwambiri kumafikira kumalekezero a dziko lapansi. Yesuyu amandionekera chaka ndi chaka. Koma m’zaka za m’ma 1980, ndinayamba kudutsa nyengo zovuta kwambiri ndipo 1984, Yesu anabwera masana, kunditenga ndi kupita nane kumwamba komanso kukandionetsa kugahena,” anatero a Zande.

Iwo anati Yesu anawauza kuti achoke mpingo wawo wa Katolika m’mawa wa tsiku lina m’chaka cha 1989, ali kumunda.

Malinga ndi a Zande, adayamba kudutsa moyo wovutandi wowawa kuchokera m’chaka cha 2006 pomwe yesu anawatengeranso kumwamba kukawaonetsa zambiri.

Koma iwo anati panali pa October 27, chaka cha 2009 pomwe Mulungu anawaonekera ndi kuwauza kuti asadye komanso kumwa madzi kwa masiku 31.

“Anandiuza kuti ndikapempherere kuphiri komwe ndinapitadi. Ndipo ndinawauza ana anga kuti azikandiona pakadutsa masiku atatu kapena 5 chifukwa mwina ndikhonza kukafa. Ndinawapemphanso kuti azibweretsa madzi oti ndizikachukuchira m’kamwa. Koma ndinavutika nditafika tsiku la nambala 8.

Ndinafooka ndipo ndinamuuza Mulungu kuti basi ndifa. Koma tsiku la chi 9, nditafookeratu, ndinaona pakatali pakubwera anyamata awiri ovala zoyera atatenga basiketi yomwe munali chakudya ndipo anandiuza kuti atate anga ndi omwe anawatuma,” analongosola a Zande.

Ndipo anati atangodya, anthuwo komanso mbale zomwe anadyera zinasowa ndipo kuchoka pomwepo anapeza mphamvu zochuluka.

“Kuchoka apo mapazi anga anatupa kwambiri ndipo anthu anayamba kunditonza mpaka ndinamupempha Mulungu kuti andiphe,” anatero a Zande.

Koma iwo anati chinali chaka cha 2013 chomwe Mulungu anawauzanso kuti azikagona m’tchalitchi chawo ndipo Mulungu anawaphanso zilakolako za thupi.

“Koma chifukwa chokhalitsa osamadya, thupi langa linayamba kuola. Moti m’miyendomu muli zipsera ngati kuti ndinapsa koma ndi chifukwa chokhalitsa m’kachisi osamadya,” iwo analongosola.

Malinga ndi a Zande, Mulungu anawauzanso kuti asale kudya masiku 40 kuchokera pa 3 March kufika pa 11 April ndipo anati unali ulendo wovuta chifukwa anafika pofooka ndikudziona kuti afa.

“Nditafika tsiku la 25 ndinaona kuti mpweya umandithera komanso ndimavutika kupuma. Ndinali pakati pa imfa ndi moyo. Koma ndinalimba mtima chifukwa ndi Mulungu anandiuza. Kuchokera tsiku lomenero ndinawauza ana kuti azindijambula ngati umboni,” analongosola motero mneneriyo.

Iwo anati akhalanso akugona pa chiguduli kuchoka 2013 kufikira chaka chatha mwezi wa May.

Malinga ndi mkulu wa mpingo wawo a Joseph Pensulo anati zimakhala zomvetsa chisoni anthu akamawaona akamaliza kusala kudya kwa masiku

ambiri osadya komanso kumwa madzi.

“Koma kusala kudya kwa ulendo uno kwa masiku 40 sikunali kophweka monga mungaonere mu zinthuzimo. Kusala kudyaku sikunali kozisangalatsa okha koma Mulungu anawatuma. Koma anthu amaona ngati ndizopanda pake,” anatero a Pensulo.

Iwo anati patatsala masiku anayi kuti amalize, anapita kukawaona ndipo chisoni chachikulu chinawagwira.

Malinga ndi a Pensulo mpingo wawo unalibe choyankhula panthawiyo koma kuvomereza kuti zitero.

Mneneri Rex Kalolo omwe ndi wamkulu wa bungwe la Prophetic Association of Malawi anati ndi bodza kuti munthu akhonza kukhala masiku 40 osadya komanso osamwa chifukwa thupi lili ndi kapangidwe kake.

“Masiku omwe munthu angadutse malinga ndi a chipatala ndi atatu ndipo Lachinayi limakhala lovuta. Timadziwa Mose komanso Yesu ndipo sitinganene zambiri chifukwa Buku Lopatulika sililongosola zambiri,” anatero a Kalolo.

Iwo anati akukaikira zoti a Zande anasala kwa masiku 40 akukaikira pokhapokha atayankha mafunso ena.

“Zimapweteketsa anthu ndi chifukwa ndimazikana nkhani zimenezi. Anthu ena amangotengera ndipo apweteketsa anthu. Palibe angakhale kwa masiku 40 osadya komanso kumwa,” anatero a Kalolo.

Iwo anati nkhanizi zikuchuluka chifukwa choti anthu ambiri alibe chidziwitso chenicheni.

“Sindikukhulupilira zimenezo malire andipatse umboni. Onse omwe anayeserapo amafa,” anatero a Kalolo.

Ndipo anati bungwe lawo likuyesetsa kulangiza anthu kuti asamachite izi chifukwa akupwetekeka nazo.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button