Nkhani

Moto lawilawi mu TNM Super League

Listen to this article

Ligi ya TNM yafika pa lekaleka pamene matimu ena akutenga mapointi ndipo ena kutaya mwachibwana pamene ligiyi tsopano yalowa sabata ya chinambala 22.

Timu ya Big Bullets yomwe idali timu yokhayo yomwe isadaone kugonja m’ligiyi yakumana ndi chakuda sabata yatha pamene idapunthidwa ndi asilikali a Airborne Rangers ku Dwangwa komwe Bullets idagonja 2-1.bullets

Kugonjaku kumadza timuyi itatibulidwa ndi Civo United m’chikho cha Standard Bank 2-1. Kodi minyamayi ipitiriranso mawa pamene timuyi ikusinjana ndi asilikali a Moyale?

Technical director wa Bullets, Billy Tewesa, adati sakuonanso akugonja m’manja mwa Moyale ndipo wati okonda Bullets abwere kudzaonera masewerawo ndipo adzasamba mkaka.

“Banja lathu lidazolowera kudyera nyama, ndiye apapa nyama inasowa ndipo timadyera masamba. Koma mukamadyera masamba si zitanthauza kuti simudzadyanso nyama.

“Pamene padavuta pakonzedwa, chilichonse tsopano chili m’chimake ndipo okonda Maule abwere Lamulungu ndipo adzamwa mkaka,” adatero Tewesa.

Mphekesera zamveka kuti timuyi ikufuna kutenga mphunzitsi wakale wa timuyi Kinnah Phiri amene wangobwera kumene kuchokera ku South Africa.

Izi zikudza malinga ndi kugonjaku ndipo lingaliro ndi lakuti timuyi iteteze ligiyi yomwe akuitsogolera ndi mapointi 41 pamasewero 18 ndipo Mafco ndiyo ikutsatira ndi mapointi 34 m’masewero 20.

Lero masewero alipolipo pamene Azam Tigers iswane ndi Be Forward Wanderers pa Kamuzu Stadium. Mumzinda wa Lilongwenso ndiye muli fumbi pamene Civo United ipumunthane ndi Silver Strikers pa Civo. Red Lions yaitana Moyale pa Zomba lero ndipo Blue Eagles yaitananso Kamuzu Barracks pa Nankhaka.

Mawa Bullets ithethetsana ndi Moyale pa Kamuzu. Fisd yomwe ili kumchira kwa ligiyi ndi mapointi 11 m’masewero 19 yaitana Airborne pa Kalulu ndipo Dedza ilandira Mafco pa Dedza

Related Articles

Back to top button
Translate »