Mwapasa autsa mapiri
Pamene pali kusamvana pakati pa aphungu a Nyumba ya Malamulo pa zovomereza Duncan Mwapasa kukhala mkulu wa apolisi m’dziko muno, akadaulo ena akuti chikhulupiiro cha Amalawi pa apolisi chidazilala.
Lachiwiri, phungu wadera la Lilongwe Mpenu Eissenhower Mkaka adatenga chiletso kuti aphungu asakambirane kaye nkhaniyo kufikira bwalolo litagamula ngati n’koyenera kuti aphungu avomereze Mwapasa. Padakalipano Mwapasa akugwirizira mpando wa mkulu wa apolisi pomwe bwana wake Rodney Jose ali kutchuthi kuyembekezera kupuma pantchitoyo.
Izi zidadza pomwe aphungu a mbali ya boma adati palibe choletsa kuvomereza Mwapasa chifukwa malamulo akupatsa mphamvu aphunguwo kutero.
Malingana ndi kadaulo pankhani za kayendetsedwe kabwino ka zinthu m’dziko Makhumbo Munthali, pali umboni woti polisi ikusoweka utsogoleri waluntha.
“Mwapasa wakhala zaka zambiri m’polisi ndipo wakhala nawo kuutsogoleri ngati wachiwiri kwa wamkulu wa polisi pomwe zoipa zina zaoneka.
“Ku mbali yanga, ndingati aphungu asavomereze Mwapasa chifukwa cha mbali yake pandale. Zimenezi zimapangitsa kuti achipani chomwe kwachokera mkulu wapolisiyo chomwe nthawi zambiri chimakhala m’boma, azigwiritsa ntchito polisi molakwika,” adatero Munthali.
Iye adati kusakhulupilirana pakati pa apolisi ndi anthu wamba kuli ndi yankho lapafupi koma longofunika nzeru za aphungu pounikira bwino pa kasankhidwe ka mkulu wa apolisi yemwe mbali yaikulu amatenga ndi mtsogoleri wa dziko.
“Ndondomeko yomwe ikufunika ikhale younika makandideti a mpando wa mkulu wapolisi osati potengera maphunziro okha kapena kuti munthuyo wakhala nthawi yaitali m’polisi, ofunikanso aziyang’ana nzeru za utsogoleri,” watero Munthali.
Mkulu wa bungwe loteteza ufulu wa anthu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) Timothy Mtambo adati bungwelo limema aphungu kuti asalole Mwapasa kukhala mkulu wa apolisi
chifukwa pamiyezi yomwe wakhala wachiwiri kwa wamkulu wa polisi komanso wogwirizira mpandowu, walephera kuonetsa ukadaulo.
“Zonse zikuchitikazi, monga anthu kuletsedwa kupanga zionetsero zomwe ndi ufulu wawo m’malamulo a dziko, kuphulitsa utsi okhetsa misozi pomwe anthu sakupanga zieaea komanso kumaonerera otsatira chipani cha DPP akuchitira nkhanza ochita zionetsero ndi kusachitapo kanthu.
“Zionetsero zakhala zikuchitika mwamtendere koma anthu otumidwa amabwera n’kudzasokoneza n’kuyamba kuthyola sitolo ndi kuba katundu wa anthu osalakwa apolisi akungoonerera, zonsezi pansi pa ulamuliro wa Mwapasa,” adatero Mtambo.
M’Nyumba ya Malamulo mpungwepungwe pankhaniyi ndiye ndi wosayamba. Zinthu zisadafike poti Mkaka n’kutenga chiletso pankhani ya Mwapasa, mudali kusinthana zichewa nkhaniyo itangoyamba mpaka Sipikala kusowa chochita n’kungogamula kuti nkhaniyo iyime kuti iye afunsire nzeru kwa otsata malamulo.
Nduna yowona za chitetezo cha m’dziko, Nicholas Dausi ndiyo idabweretsa nkhaniyo koma mtsogoleri wa mbali yostutsa boma m’nyumbayo Lobin Lowe adati nkhaniyo isapitilire chifukwa mkulu wapolisi alipo kale, kunena Jose.
“Tivomereza bwanji mkulu wapolisi wina pomwe winayo akadali pampando kutengera malamulo?” adatero Lowe.
Koma nduna ya zamalamulo Bright Msaka adati malamulo omwewo amati ngati mwini ofesi m’boma wapita ku tchuthi ndipo pobwera kumeneko adzafikira kupuma pantchito yake, munthu wina akhoza kusankhidwa n’kulowa mmalo mwake.
Msaka amagwiritsa ntchito gawo 30 (1) ya malamulo a dziko lino koma Mkaka adagwiritsa ntchito Gawo 4 ya malamulo omwewo ponena kuti malamulo amamanga nthambi zonse za boma pa mlingo uliwonse moti palibe chomwe angachitepo.
Sipikala wa nyumbayo Catherine Gotani Hara ataona kuti mbali zosiyanasiyana zikubwera ndi magawo onena zotsutsana a malamulo, adangogamula kuti nkhani ya Mwapasa iyambe yaima mpaka atafunsira nzeru kwa akadaulo pa zamalamulo.
Nkhaniyo isadafike konseku, padatuluka maganizo osiyanasiyana kuchokera kwa atsogeri a mbali zosiyanasiyana m’nyumbayo.
Mkaka adati Mwapasa alibe mapepala omuyenereza pa mpandowu. Ndipo mtsogoleri wa UDF m’nyumbayo Lillian Patel adati aphungu asayang’ane kochokera kwa munthu pokambirana za Mwapasa.
Mkulu wa PP m’nyumbayo John Chikalimba adagwirizana ndi Patel kuti nkhaniyi isakhudze kochokera kwa munthu.
Wachiwiri kwa wapampando wa komiti ya zosankha anthu m’mipando (Public Appointments Committee) Rachel Mazombwe Zulu adati komitiyo idapeza kuti Mwapasa ali ndi zomuyenereza zonse kukhala mkulu wa apolisi.