Jannah Theme License is not validated, Go to the theme options page to validate the license, You need a single license for each domain name.
Nkhani

Njala saweta, atero kadaulo

Kadaulo pa za malimidwe ndi kuonetsetsa kuti anthu ali nchakudya chokwanira a Tamani Nkhono-Mvula aunikira boma kuti lisamalote pa mpando za nkhani yokhudza chakudya.

Lipoti la kamlosera wakapezekedwe ka chakudya wachaka lomwe lidatuluka Lamulungu likusonyeza kuti anthu oposa 4 miliyoni akhala ndi njala kutsatira kusakolola moyenera pazifukwa zingapo.

Polankhula ndi Tamvani kutsatira mawu a nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi ya DoDMA kuti iyamba kusaka thandizo la chakudya chogawira anthu omwe alibe chakudyawo, a Mvula ati m’dziko muno timachita zinthu mwachibwana.

“Zoona azitiuza kuti ayamba kusaka thandizo lero? Chomwe timachitachi n’chibwana chifukwa chakudya sichoseweretsa ayi. Ku nkhokwe kumayenera kuzikhala chimanga nthawi zonse kupangira nyengo ngati iyiyi,’’ atero a Nkhono-Mvula.

Iwo ati tsogolo la dziko pa chakudya limadziwika ngakhale alimi asadakolole kutsatira kauni woyamba ndi wachiwiri wakakololedwe ndiye nzomvetsa chisoni kuti boma lizifika mwezi ngati uno lilibe pogwira.

“Tizikhala ngati anamwali asanu a nzeru, kukonzekeratu osadikira kuti mphepo iwombe ndiye tizitanganidwa ayi. Njala nchilombo saweta. Ndalama zomwe zikufunika n’zambiri ndiye funso n’kumati azitenga kuti lero ndi lero?’’ Atero a Mvula.

Iwo ati dziko loika mtima  pa miyoyo ya nzika zake silingalekerere nkhokwe zake zilibe chimanga kwamiyezi yoposa itatu chifukwa zinthu zikavuta, maso a anthu amakhala Ku nkhokwe zaboma.

Nthambi ya DoDMA yati ikufuna ndalama zokwana K387.20 biliyoni zoti igulire chimanga chokwana matani 200 000 a chimanga chogawira anthu omwe alibe chakudya.

Mneneri wa DoDMA a Chipiliro Khamula adati, lipotilo lidawatsegula mmaso kuti ayambe kuyang’ana thandizo lachakudya.

“Apapa zakhala bwino chifukwa tadziwa njira, tsopano tiyamba kusaka thandizo limodzi ndi abwenzi athu kuti anthu asavutike ndi njala,” adatero a Khamula.

Woyang’anira zakagwiritsidwe ntchito kabwino kazinthu kubungwe la Center for Social Concern Mayi Agness Nyirongo agwirizana ndi a Mvula kuti mpofunika kumakonzekera chakudya cha chaka chamawa mmbuyo muno.

‘’Timayenera kumaphunzirapo pazomwe tadutsamo kale, sizachilendo kuti kuno timakhala ndi njala ndiye njira yabwino nkumasonkhetsa thandizo lachaka chotsatira osati lachaka chomwecho,’’ atero a Nyirongo.

Amalawi ena ati ngati chimanga kulibe, boma lisazengeleze kuvomeleza kuti othandiza abwele msanga komanso zithandiza kuti Amalawi asapinde manja koma azitakataka kuti apeze chakudya.

‘’Chaka chatha, boma lidachedwa kuvomera ndipo zotsatira zake, ngakhale chimanga chidagawidwa, mmadera ena sichidafike ndipo limeneli likhale phunziro kuyambira panopa,’’ atero a Ian Kefasi aku Area 38 ku Lilongwe.

Pokonzekera nyengo ya njala, boma lidakhazikitsa ndalama zokwana K99.5 biliyoni yaulimi wamthilira komanso lidatsegula msika wa mbewu wa Admarc msanga kuti boma ligule chimanga chokwanira.

Koma a Gift Kakunja aku Kauma m’boma la Lilongwe ati alimi ambiri adagwira chimanga chawo kaamba kamitengo kuwopa kupanga maluzi akawelengera zolowa monga fetereza.

Dziko la Malawi limafunika chimanga chokwana matani 3.7 miliyoni yachakudya kuti mdziko musakhale njala koma chaka chino, dziko lonse lidakolola matani 2.9 miliyoni kutanthauza kuti pali gwelu lofunika kutseka.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button