Nkhani

Nkhanza zapolisi zanyanya

Listen to this article

Ophunzira 24 a kusukulu za ukachenjede apereka maina awo ku bungwe la maloya la Malawi Law Society (MLS) za nkhanza zimene achitiridwa panthawi yomwe amachita zionetsero zokwiya ndi kukwera mtengo kwa fizi.

Iwo adachita izi MLS itawapempha kuti apereke mainawo potsatira nkhanza zimene apolisi adachitira ophunzirawo amene akwiya kuti fizi zakwera kuchokera pa K275 000 kufika pa K400 000.

Apolisi kuponda mwana akufuna kutolera mabotolo ku Kamuzu Stadium
Apolisi kuponda mwana akufuna kutolera mabotolo ku Kamuzu Stadium

Nkhanzazo zidafika pambalambanda kwambiri ena atajambula pa vidiyo wapolisi wina ataomba khofi wophunzira wa chaka cha chinayi Mayankho Kapito, yemwe ndi mwana wa mkulu wa bungwe loona zaufulu wa anthu ogula la Consumers Association of Malawi (Cama) John Kapito. Kapito wati asumira apolisiwo.

Mtsogoleri wa ophunzira ku Chancellor College Ayuba James adatsimikiza kuti pofika Lachitatu chiwerengero cha ophunzira omwe adapereka maina awo adali atafika pa 24.

“Talandiradi mainawo koma tikudziwa kuti chiwerengero chayenera kukhala chokwera kwambiri chifukwa ambiri apitapita m’makwawo. Nkovuta kuti uthengawu uwafikire,” adatero James.

Chikalata cha MLS chidapempha ophunzira amene angakhale ndi umboni wa nkhanzazo kuti apereke maina awo. Ngakhale mneneri wa bungwelo Khumbo Soko adatsimikiza za ntchitoyo, adakana kuthirirapo ndemanga chifukwa ati akadali mkati mopeza mainawo.

Nthawi ya zionetsero za ophunzirawo, apolisi akhala akumenya ophunzirawo ndipo amangapo angapo pa zipolowe zomwe zakhala zikuchitika m’sukulu zomwe zili pansi pa University of Malawi (Unima).

Izi zili apo, mabungwe ena a zaufulu wa Amalawi ati nkhanza zankitsa kupolisi ndipo ati izi zikusemphana ndi zimene amalengeza kuti adasintha.

Sabata yatha, dotolo wodziwika bwino Dr Frank Taulo adalemba pa Facebook kuti adapeza apolisi akumenya anthu amene adawapeza akungoyenda mu Limbe mumzinda wa Blantyre nthawi itangokwana 6 koloko madzulo.

“Nditawafunsa chifukwa chiyani amamenyera anthuwo, adandikuta. Nditawauza kuti ndine wakuti, sadalabadire ndipo adandionongeranso galimoto langa,” adatero Taulo.

Posakhalitsapa, mwini malo ena a chisangalalo ku Chigumula mumzindawu, Sharat Gondwe adatinso apolisi adamumenya atabwera kudzatseka malo akewo, Pitchers’ Club.

Anthu ena amene tidacheza nawo ku Lilongwe nawo adasimba za nkhanza za apolisi. Gift Potani wa kumsika wa ku Area 24, Andrew Mwenye wa mumsika wa Tsoka komanso Alinafe Matthias wa ku Area 22 adanena kuti apolisi akumanga anthu kapena kuwakwapula kumene opanda chifukwa chenicheni.

“Nthawi zina amapeza anthu malo omwera masanasana nkuwaphaphalitsa, ena kutengedwa osapatsidwa mpata wofotokoza zomwe akuchita,” adatero Potani.

Si ana a sukulu kapena Amalawi wamba amene akudandaula za nkhanzazi. Nawo amayi oyendayenda ati amakumana ndi nkhanza za apolisi akagwidwa pantchito yawoyi.

Mneneri wa bungwe loyimilira amaiwa, Zinenani Majawa, adati pakati pa apolisi pali Chichewa choti ‘Dzipulumutse’ kutanthauza kuti wogwidwayo apereke kena kake kapena akakhala mzimai asinthitse thupi lake ndi ufulu.

“Apolisi akatigwira vakabu amati dzipulumutse wekha kutanthauza kuti akufuna ndalama ndipo ngati palibe amamumenya kapena kumugona mzimai popanda chitetezo chilichonse ndiye poti ndi wapolisi, kokanena kumasowa,” adatero Majawa.

Mkulu wa bungwe la zaufulu la Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR) Timothy Mtambo adati apolisi akadaunika mofatsa magwiridwe awo antchito kuti pomwe akuteteza miyoyo ndi katundu, asamaphwanye ufulu wa ena.

Mneneri wa apolisi m’dziko muno Nicholas Gondwa adaikira kumbuyo apolisi ndipo adati akugwira ntchito yawo potsata malamulo. Mawuwo adadza pomwe apolisi adalengezanso kuti akufufuza za wapolisi wothyapa khofi mwana wasukulu.

“Tikafika poponya utsi okhetsa misozi ndiye kuti zionetsero zafika pa zipolowe pofuna kuteteza anthu amene sizikuwakhudza ndi katundu wawo. Komanso kumanga ena mwa anthuwo kumakhala kuziziritsa zipolowezo,” adatero Gondwa.

Iye adati apolisi akafika pamalo ena, amakhala kuti awuzidwa kuti pali zigandanga zine zimene akuzisaka ndiye nthawi zina ena amene sizikuwakhudza amangoyamba kuthawa nawo. “Timawagwira kuti akafotokoze chimene amathawa,” adatero Gondwa. n

Related Articles

Back to top button
Translate »