‘Osatengeka ndi mabokosi’
Anthu ena a m’dera la kummwera mu mzinda wa Blantyre achenjeza ovota m’deralo ngakhalenso dziko la Malawi kuti akhale osamala povota pa chisankho chikubwerachi posatengeka ndi zinthu zimene si za phindu kwenikweni koma zimangofuna kuwaphimba mmaso.
Mmodzi mwa anthuwo a Chris Magwira ati anthu sakuyenera kusankha anthu chifukwa choti omwe akufuna mpando wa uphungu kapena ukhansala akuwagulira mabokosi a maliro chifukwa uku n’kulemekeza anthu akufa mmalo mwa amoyo.
“Sindikunena kuti tisamalemekeze maliro ayi komatu anthu ayenera kudziwa kuti nthawi ya kampeni amabwera ena ndi njira zawo monga kutsegula malo oti anthu azikatenga mabokosi mwaulere. Kwa ine amene angabwere ndi chitukuko cha chipatala kuti mmalo moti anthu azifa kaamba ka kusowa thandizo, izi zizikhala zopezekeratu,” atero a Magwira.
Iwo adati mwachitsanzo pa zaumoyo deralo likufunika zinthu za makono kuti anthu asamavutike.
“Taona mmbuyomu phungu akugwira ntchito za chitukuko pomanga mlatho wopita ku chipatala chaching’ono cha Zingwangwa komanso kukonza malo okhala odikirira odwala ku chipatala cha Gulupu chimene chili m’dera lino. Zimenezo ndi zomwe tikufuna,” adatero a Magwira.
Malinga ndi a Aubrey Wadidi achinyamata m’deralo komanso kulikonse m’Malawi kuti asatengeke ndi andale ongolonjeza mwayi wa ntchito ngakhalenso kuti miyoyo yawo ipite patsogolo ndi kukhala koma osakwaniritsa kanthu.
“Ndife onyadira kuti kuno kuli Zingwangwa Youth Centre zimene mataunishipi ambiri mu mzinda wa Blantyre alibe. Timathokoza phungu amene adalipo mmbuyomu a Allan Ngumuya amene adamenyerera kuti malowa akhazikitsidwe. Ndiponso iwo adatsegula malo ambiri m’tauni ya Blantyre komwe achinyamata omwe adalibe mwayi wa ntchito kuti azipukuta nsapato za anthu,” adatero iwo.
Iwo adati amanyadira kuti Zingwangwa ndi Bangwe ndi mataunishipi okhawo amene ali ndi malo a achinyamata otere mu mzinda wa Blantyre. Kumeneko, pa mbali pa masewero ndi msangulutso, kumachitikiranso misonkhano yofunika monga tsiku lokumbukira za matenda a Edzi.
Ku mbali yawo, a William Zgambo, omwe ati anthuwo ali m’gulu la Friends of Allan Ngumuya, adati akukumbukira kuti nthawi yake, phunguyo ankaonetsetsa kuti aliyense akugula chimanga mopanda mavuto kwenikweni.
“Ankaonetsetsa kuti pasakhale wolowerera pogula chimanga. Izi ndakumbukira kwambiri chifukwa pano anthu akung’wempha ndi njala chifukwa m’misika ya Admarc zinthu sizikuyenda. Ngakhale chimanga chochepa chitakhalapo, zikungothera kwa a ndalama,” adatero iwo.
Iwo adati posachedwapa ayesetsa kuti asake phungu wakaleyo kuti mwina n’kulingalira zodzaimanso pa chisankho chikudzachi.