Nkhani

Patrick Mwaungulu ndi katakwe pokankha chikopa

Listen to this article

Patrick Mwaungulu ndi mnyamata wachichepere koma wa luso lalikulu pokankha chikopa ku timu ya Nyasa Big Bullets. Mwaungulu anasankhidwa ngati wosewera mpira bwino kwambiri mu timuyi mwezi wa June ndipo analandira K100 000. Tinacheza ndi Patrick motere:

Tikudziweni?

Ndine Patrick Mwaungulu, ndili ndi zaka 20. Ndimakhala mzinda wa Blantyre.

Patrick sakubwerera mmbuyo pa chikopa

Kodi maphunziro mudafika nawo pati?

Sukulu yanga ya pulaimale ndinaimba pa Chiwavi pomwe ya sekondale ndinaphunzira pa sekondale sukulu ya Chiwavinso mzinda wa Mzuzu.

Nanga mumatani pa moyo wanu?

Ndine wosewera mpira. Ndipo nthawi yanga yambiri ndimakhala ku mpira.

Mudayamba bwanji luso lanu la mpira?

Ndidayamba ndili sitandade 3 ndipo ndinkangosewera ngati masewera chabe. Koma pakupita pa nthawi, ndili Folomu 3 ku sekondale, ndinasankhidwa kukasewera ku timu ya dziko lino ya osewera osadutsa zaka 17.

Apa tinapita kunja ndinakachita bwino. Panthawiyo ndinali ndikusewera mu timu ya Sanwecka ya osewera osadutsanso zaka 17.

Ndikuchoka uko, anandikweza ndipo ndinayamba kusewera mu timu yaikulu ya Sanwecka ya osewera osapitilira zaka 20. Ndinangomenya nayo ligiyo ulendo wachiwiri, ndipo pomwe umati ulendowu ukutha, timu ya Nyasa Big Bullets-Reserve inanditenga kwa zaka 5.

Nditasewera mpira ku Reserve kwa zaka 4, pakadali pano anandisankha kusewera ku timu ya Nyasa Big Bullets-yaikulu. Ndili mu chaka changa choyamba.

Ndi mavuto otani omwe mumakumana nawo pa ntchito yanu?

Mavuto akulu amakhalapo munthu akavulala chifukwa akachira zimakhala zovuta kubwerera mu timu malinga n’kuti nthawi zina amnzako omwe akusewera m’malo mwako amakhala akusewera bwino kwambiri choncho zimakhala zovuta kuti ubwererenso bwino, msanga.

Nanga mumathana nawo bwanji?

Kulimbikira kuti ubwererenso mu timu, kuona zofooka za amnzakowo ndikuzikonza komanso kumvera otiphunzitsa mpira.

N’chiyani chomwe mumafuna chitasintha kuti luso lanu lipite patsogolo?

Timafuna thandizo kuti zinthu zizipita pa tsogolo chifukwa pamakhala zina zosowekera zomwe zimafunika kuti anthu azikuthandiza nthawi zina.

Mungamulimbikitse bwanji munthu amene akufuna kutsata mapazi anu?

Chofunika kwambiri ndi kulimbikira, kudzichepetsa komanso kumvera aphunzitsi a mpira. Komanso kulimbikira kupemphera chifukwa Mulungu ndi amene amapatsa.

Kodi muli pa banja?

Sindili pa banja. Ndidakali wachichepere, ndikukonza kaye tsogolo pano.

Mawu anu wotsiriza ndi wotani?

Anthu onse onditsatira, apitilize kundikonda nthawi yabwino komanso yoipa.

Related Articles

Back to top button
Translate »