Nkhani

Sakufuna awakanize kuima

Mamembala ena a chipani cha Malawi Congress (MCP) akutsutsana ndi maganizo amene komiti yaikulu ya chipanicho (NEC) idamanga kumsonkhano wake.

Komitiyo idamanga zoti mamembala ofuna kudzapikisana nawo m’maudindo a m’komiti yaikulu ya NEC ku konvenshoni ya mwezi wa August 2024 adzakhale woti wakhala membala wa chipani kwa zaka zoposa ziwiri.

A Njobvuyalema: Komiti siyidaphwanye malamulo

Koma mamembala ena a chipanicho atsutsa mfundoyo ndipo ena mwa iwo ayamba kale kukambirana ndi kufunsa nzeru kwa maloya ngati mfundoyo ili yogwira.

Mmodzi mwa okhudzidwawo a Eddie Banda omwe akufuna kudzaimilira ngati wachiwiri kwa oyang’anira za mamembala m’chipani ati alembera kale kalata yokhudza nkhawa zawo mlembi wamkulu a Eisenhower Mkaka.

Mwa zina, a Banda alongosola m’kalata yawoyo kuti atsogoleri akuluakulu a chipani monga mtsogoleri woyamba a Hastings Kamuzu Banda, mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera komanso mlembi wamkulu wakale a Chris Daza adatenga maudindowo posagwiritsa ntchito mfundo imeneyi.

Wapampando wa chipanicho m’boma la Nkhata Bay a Manase Chiumia komanso wapampando wa chipanicho ku Mwanza a James Kasamwe ndi ena mwa omwe anena poyera kuti sakugwirizana ndi mfundoyo.

Mkhalakale m’chipani cha MCP a Joseph Njobvuyalema ati ngakhale mfundoyo ili yatsopano, komiti yaikuluyo siyidaphwanye lamulo lililonse koma adati mfundozo n’zofunika akazipereke ku konvenshoni kuti nthumwi zikakambirane.

Kadaulo wa za malamulo a Gladson Majekete adati chikhoza kukhala chinthu chomvetsa chisoni kwambiri ngati chipani cha MCP chingayambe kugwiritsa ntchito mfundozo zisadaunikidwe ku kovenshoni.

“Atsogoleri amakhala ndi mphamvu zochita ziganizo koma nthawi zina mphamvu zimenezo sazigwiritsa ntchito bwino. NEC ikhoza kupanga mfundo koma ikuyenera kuzindikira kuti chipaninso chili ndi malamulo oyenera kutsatidwa,” adatero a Majekete.

Pakatipa, chipani cha MCP chakhala chikulandira mamembala osiyanasiyana ochokera m’zipani zina makamaka cha Democratic Progressive Party (DPP) omwe adali m’maudindo akuluakulu kuzipani zawo zakale.

Ena mwa akuluakulu omwe adachoka m’chipani cha DPP komwe adali ndi maudindo akuluakulu ndi a Uladi Mussa omwe adali wachiwiri kwa Pulezidenti wa DPP pachigawo cha pakati, a Esther Mcheka Chilenje omwe adakhalapo sipikala wa Nyumba ya Malamulo mwa ena.

Koma polankhulapo pa nkhaniyi, mneneri wa chipani cha MCP a Ezekiel Ching’oma adangoti chipani chawo chili ndi ndondomeko zomwe chimatsata koma adalonjeza kuti atsogoleri a chipanicho akumana ndipo atulutsa kalata yofotokoza momwe aziyendetsere.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button