Dikirani kauniuni wachiwiri wa mbewu
Unduna wa za malimidwe wati anthu asathyolere khosi zotsatira za kauniuni woyamba wa mbewu chifukwa kauniyo sadalingalire za ng’amba yomwe idagwa pafupifupi mwezi onse wa February.
Nduna ya za malimidwe a Sam Kawale anena izi pomwe amasanthula mapulani omwe boma lakonza kuti lidzachepetse vuto la chakudya ngati ng’ambayo ichepetse kakololedwe.
Sabata yatha, undunawo udatulutsa zotsatira za kauniuni woyamba yemwe adasonyeza kuti dziko lino lidzakolola chimanga chokwana matani 3 608 862 poyerekeza ndi matani 3 509 837 omwe tidakolola chaka chatha.
Koma pothirirapo ndemanga, anthu ambiri adaikapo mlomo kuti ili ndi bodza la mkunkhuniza, potengera kuti chimanga chambiri m’mindamu chidauma ngati anyezi kaamba ka ng’amba yodza ndi nyengo ya El Nino.
Koma a Kawale adati: “Zotsatirazi n’zakauni woyamba yemwe amachitika alimi akangobzala kumene ndiye amaunikira zinthu monga kulandira kwa malo omwe alimi alima komanso kuchuluka kwa mbewu zomwe zabzalidwa.
“Pakatipa kudagwa ng’amba ya pafupifupi mwezi watunthu ndiye n’kutheka kuti kauni wachiwiri akhoza kudzapeza kuti tikolola zocheperako kaamba ka ng’ambayo ndiye tidikire kauni winayo,” atero a Kawale.
Kauni wa kakololedwe amachitika katatu chaka chilichonse ndicholinga chofuna kupereka chithunzithunzi cha momwe anthu akololere mbewu zosiyanasiyana monga chimanga, soya, thonje, fodya ndi zina zotero.
A Kawale ati polingalira chiopsezo chomwe ng’amba ingabweretse ku dziko lino, boma layamba kale kugwira ntchito ndi alimi akuluakulu kuti alime chimanga chambiri cha mthirira.
Sabata zapitazo, andunawo adali kalikiliki kuyendera ina mwa mindayo nkumagawana nzeru ndi eni ake za momwe alimiwo angagwirire bwino ntchito ndi boma kuti alime chimanga chambiri.
Mmodzi mwa alimi akuluakuluwo a Jimmy Koreia Mpatsa omwe adapanga ubale ndi boma kudzera ku Greenbelt Authority n’kutsegula Mpatsa Greenbelt Mega Farms Ltd ati pano akulima chimanga cha mbewu choti adzabzale m’chirimwe.
A Mpatsa adati njira yomwe boma latsata yolimbikitsa ulimi wa mthirira ndi yankho labwino loonetsetsa kuti m’dziko muno mukhale chakudya chokwanira.
“Vuto lalikulu ndi loti nyengo siyipanganika, mwachitsanzo, mvula itha kuyamba bwino kenako n’kudula ngati momwe zakhalira chaka chino ndiye yankho lodalirika ndi mthirira basi,” adatero a Mpatsa.
Nalo bungwe la Farmers Union of Malawi (FUM) lati alimi ayambiretu kukonzekera ulimi wa mthirira monga kusonkhanitsa zipangizo komanso asadzapupulume kugulitsa zomwe angadzakolole.
Mkulu wa bungwelo a Jacob Nyirongo ati alimi ang’onoang’ono ndiwo amadyetsa dziko koma nthawi zambiri njala ikagwa alimi ngati omwewo ndiwo amakhudzidwa kwambiri.
“Tikulimbikitsa njira ziwiri, njira yoyamba alimi adzasamale zomwe adzakolole kuti adzakhale ndi chakudya chokwanira. Njira yachiwiri, ayambiretu kukonzekera mthirira kuti ngati n’kugulitsa adzagulitseko chamthiriracho atasunga chakudya chokwanira,” atero a Nyirongo.
Lipoti la kauni woyambayo likusonyeza kuti alimi ambiri adathamangira ku chimanga kaamba kokopeka ndi mtengo wake pa msika koma kaamba ka ng’amba, chimanga chambiri chidafulira pafupi kapena kufoteratu kumene.
Chaka chino, Amalawi oposa 4.5 miliyoni akusowa chakudya chifukwa chaka chatha sadakolole bwino ndipo kupatula kulimbukitsa mthirira, boma laika padera K12 biliyoni yoti kampani ya Admarc idzagulire chimanga.