Nkhani

Tambala walira

Listen to this article

Chipani cha Malawi Congress  Party (MCP) chapeza mipando 4 mwa mipando 7 ya aphungu yomwe zipani komanso oima paokha amalimbirana pachisankho chobwereza chomwe chidachitika Lachiwiri.

Pamipandoyo, MCP yateteza mipando yomwe idali yake kale ya kumwera kwa Nsinja ku Lilongwe ndi kumpoto kwa Ntchisi ndipo yatsomphola mipando yomwe idali ya Democratic Progressive Party (DPP) ya pakati ku Nsanje komanso kumpoto kwa bomalo.

Anthu adaponya voti m’madera ena Lachiwiri

Mipando ina ya aphungu pachisankhocho yapita ku UTM mpando umodzi wa kumpoto cha kumadzulo kwa boma la Karonga pomwe United Democratic Front (UDF) yateteza mpando wake kummawa kwa Chikwawa ndipo woima payekha Bizwick Million watenga mpando wa ku Zomba Changalume.

Chipani chongotuluka kumene m’boma cha DPP chatenga mipando yonse iwiri ya makhansala ku Livilidzi ku Balaka komanso Chitakale ku Mulanje.

Akadaulo pa ndale ati zotsatirazo n’zosadabwitsa makamaka pachipani cha DPP chomwe chikudziweyesa chokha kaamba ka mikangano yokhudza utsogoleri yomwe ili m’chipanimo.

 Boniface Dulani wa ku Chancellor College wati ngati DPP siyisintha machitidwe a ndale zake, isadzadabwe itatha kufika pa UDF yomwe idalamulako kwa zaka 10 ndipo idali ndi mphamvu zoopsa.

“Apapa atengerepo phunziro kuti akapanda kusintha basi akupita. Chodandaulitsa nchoti dziko lino likufunika mbali yotsutsa ya mphamvu ndipo chiyembekezo padakalipano chili mwa DPP,” adatero Dulani.

Kadaulo winanso Happy Kayuni adati ndi zomwe zachitika pachisankhochi, chipani cha DPP chikuyenera kuitanitsa msonkhano waukulu msanga kuti chikasankhe utsogoleri wina omwe ungakwanitse kumanga chipani.

“Awawa ngati sachititsa kovenshoni msangamsanga, adziwiretu kuti chawo palibe mu 2025. Mapokoso omwe ali m’chipanichi akula kwambiri ndipo alowetsa nthenya,” adatero Kayuni.

Koma mneneri wa DPP Brown Mpinganjira samayankha lamya yake kuti alankhulepo za momwe chisankho chayendera.

Woyendetsa kampeni m’chipani cha MCP Moses Kunkuyu adati kupambana kwa chipanicho pachisankho chobwereza makamaka polanda mipando kumwera n’chitsimikizo choti chipani tsopano chamera mizu paliponse.

“Nanga mufuniranji umboni wina? Aliyense waona momwe chisankho chayendera ndipo pali umboni waukulu kuti MCP n’chipani chokondedwa. Mukaonanso komwe taluza, timangosiyana pang’ono ndi wopambanayo,” adatero Kunkuyu.

Pomwe mlembi wamkulu wa UTM Patricia Kaliati adati chipani chawo chayesetsa potengera kuti chidalibe zipangizo zokwanira za kampeni poyerekeza ndi anzawo omwe amapikisana nawo.

“Komabe ndine wokondwa kuti Amalawi aonetsa kuzindikira kuti ngakhale wina asakhale ndi zipangizo koma ngati ali ndi mfundo zabwino, oyenera ndi ameneyo,” adatero Kaliati.

Kumpoto cha kumadzulo kwa Karonga wapambana ndi Felix Katwaff Kaira wa UTM, kumpoto kwa Ntchisi ndi Arnold William Kanjadza wa MCP, kumwera kwa Nsinja ku Lilongwe watenga ndi Francis Belekanyama wa MCP, Zomba Changalume Bizwick Million woima payekha pomwe kummawa kwa Chikwawa ndi Rodrick Sam Khumbanyiwa wa UDF. Kumpoto kwa Nsanje wapambana ndi Masautso Chizuzu wa MCP pomwe Nsanje Kafandikhale Mandevana wa MCP.

Lucius Elia wa DPP watenga mpando waukhansala kuwodi ya Livilidzi pomwe Richard Mulingano wa DPP watenga mpando waukhansala kuwodi ya Chitakale.

Kumpoto kwa Karonga chisankho chidabwerezedwa potsatira imfa ya James Kamwambi yemwe adali wa DPP, ku Nsinja chisankho chidadza potsatira imfa ya Lingson Belekanyama wa MCP, ndipo kumadzulo cha kumpoto kwa Ntchisi kudali chisankho chifukwa cha imfa ya Jacqueline Chikuta wa MCP komanso ku Zomba Changalume potsatira infa ya John Chikalimba wa PP.

M’madera ena monga kumpoto kwa Nsanje komwe kudali Esther Mcheka Chilenje wa DPP, pakati pa bomalo komwe kudali Francis Kasaira wa DPP ndi kummawa kwa Chikwawa komwe mwini wake Rodrick Khumbanyiwa wa UDF wapambananso, chisankho chidabwerezedwa chifukwa khothi lidagamula kuti chichitikenso litapeza kuti sizidayende bwino mu 2091.

Zisankho za makhansala zidachitika ku Livilidzi potsatira imfa ya Nelson Chimera komanso ku Chitakale potsatira imfa ya Owen Kampira.

Mkulu wa bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) Chifundo Kachale adati ngakhale m’madera ena mudali zachipolowe monga ku Lilongwe ndi Nsanje, zisankhozo zidayenda bwino.

“Tidalandira malipoti a zipolowe ku Lilongwe Nsinja komanso Nsanje koma zonse zili m’manja mwa apolisi monga mwa ntchito yawo ya chitetezo,” adatero Kachale.

Iye adati pampikisano wa aphungu padali amayi 9 ndi abambo 30 pomwe pampikisano wa khansala padali abambo 9 popanda mayi komanso adati achinyamata amangooneka nthawi ya kampeni basi.

Zipolowe za pakati ku Nsanje zidayamba pomwe a chipani cha MCP amaganizira a DPP kuti amakatenga anthu odzavota ku Mozambique.

Related Articles

Back to top button