Nkhani

Tidasiya kugwira vakabu—apolisi

Listen to this article

Apolisi ati adasiya kugwira vakabu khoti litagamula kuti mchitidwewu umaphwanya ufulu wa anthu.

Mneneri wa polisi James Kadadzera watsutsa zomwe anthu ena a mu mzinda wa Lilongwe auza Msangulutso kuti apolisi akuwagwirabe vakabu.

Kadadzera: Anthu akusokoneza

“Ili ndi bodza lankunkhuniza. Tidasiya kugwira vakavu mogwirizana ndi chigamulo cha khoti lalikulu ku Blantyre choti vakabu ndi kuphwanya ufulu wa anthu,” adatero Kadadzera.

Matthews Dziyenda, yemwe amagulitsa kaunjika mu mzinda wa Lilongwe, adauza Msangulutso kuti posachedwapa apolisi adamugwira vakabu.

“Apolisi anandigwira vakabu ndikugulitsa kaunjika ku malo okwerera basi m’tauni ya Lilongwe mpaka adandilipitsa ndalama, sadanditengere ku khoti,” adatero Dziyenda.

Kasunda: Timagwira ntchito ndi apolisi

Naye Lukas Maulidi wa  mu mzinda womwewo adati posachedwapa adagwidwa vakabu.

“Ndimadikira minibasi yopita ku Ngwenya ndipo ndidangoona anzanga akuthawa. Pomwe ndimati ndicheuke, ndidangozindikira ndili m’manja mwa apolisi.

“Adanditengera ku polisi ya Area 3 komwe adandiuza kuti ndapezeka malo osayenera nthawi yotaika,” adatero Maulidi.

Anthu angapo omwe Msangulutso udalankhula nawo adatsimikiza kuti apolisi akugwirabe vakabu.

Koma Kadadzera adati anthu omwe apolisi amagwira amakhala atapalamula milandu ina osati vakabu.

Iye adati nthawi zina makhonsolo amapempha apolisi kuti awathandize kugwira anthu omwe akuchita malonda m’malo osavomerezeka.

“N’kutheka anthu akusokoneza vakabu ndi chiseso chomwe timapanga ndi makhonsolo osiyanasiyana a m’dziko muno.

“Timatha kulowa m’tauni kapena m’dera ndi kumafufuza katundu wobedwa. Timafunsa anthu kuti ationetse malisiti akatundu wawo.

“Chiseso chimathandiza chifukwa ena amapezeka ndi katundu wobedwa pamene ena amapezeka ndi katundu woletsedwa monga chamba. Choncho anthu asasokoneze valabu ndi chiseso,” adatero Kadadzera.

Mneneri wa khonsolo ya Blantyre, Anthony Kasunda ndi wa Mzuzu, Karen Msiska, adavomera kuti nthawi zina amagwira ntchito ndi apolisi.

“Imene ija si vakabu koma kukonza mzinda. Cholinga chake ndi kuchotsa amalonda m’malo osayenera,” adatero Kasunda.

Mneneri wa makhoti, Mlenga Mvula, adati malamulo amapereka mphamvu kwa makhonsolo kuthamangitsa wabizinesi aliyense yemwe akugulitsa katundu wake pam’malo wosavomerezeka.

Bwalo lalikulu la milandu mu mzinda wa Blantyre chaka chatha lidagamula kuti vakabu ithe Mayeso Gwanda atakasumira apolisi omwe adamufinya usiku.

Related Articles

Back to top button