Tikwanitsa lonjezo lililonse—Chakwera
Mtsogoleri wadziko lino Lazarus Chakwera wati Amalawi asamvere za anthu omwe akufalitsa kuti boma lake lafotsera malonjezo omwe lidapereka pa nthawi yakampeni.
Chakwera adanena izi poyankha funso la phungu wa kumwera cha kumadzulo kwa boma la Nkhata Bay Noah Chimpeni yemwe amafuna kuti afotokoze malonjezo omwe boma lake laika patsogolo pa en. onse.
Iye amakaonekera kachitatu ku Nyumba ya Malamulo chitengereni mpandowo kukayankha mafunso osiyanasiyana a aphungu.
Poyankha funso la Chimpeni, Chakwera adati boma la Tonse Alliance lidayamba kale kukwaniritsa malonjezo omwe adali ofunika kwambiri ndipo ena onse azikwaniritsidwa malingana ndi nthawi.
“Pasakhalenso nkhawa iliyonse yokhudza malonjezo chifukwa boma ilili likwaniritsa lonjezo lililonse lomwe lidaperekedwa koma nthawi ndiyo izinena malingananso ndi kufunika kwa lonjezolo,” adatero Chakwera.
Iye adatchula pulogalamu ya zipangizo zaulimi zotsika mtengo ya Affordable Inputs Programme (AIP), kukweza ndalama zoyambira malipiro kufika pa K50 000 komanso kuonjezera malipiro osayenera kudula msonkho kufika pa K100 000.
“Malonjezo awawa sakadadikira chifukwa akukhudza miyoyo ya Amalawi monga kukhala ndi chakudya chokwanira komanso kukhala ndi ndalama kuti moyo wawo uziyenda bwino,” adatero Chakwera.
Iye adadandaula kuti anthu ena amapupuluma kudzudzula kuti zinthu zikuchedwa kuiwala kuti zonse sizingatheke nthawi imodzi.
Mabungwe omwe siaboma akhala akudzudzula Chakwera ndi boma la Tonse Alliance kuti akuchedwa kukwaniritsa zomwe adalonjeza pa kampeni kapena kupeleka ndondomeko yamomwe bomalo likwaniritsile malonjezowo.
Mkulu wa bungwe la Centre for Democracy and Economic Development Initiative (Cdedi) Silvestre Namiwa adapempha Chakwera kuti asayiwale malonjezo omwe adamuika pampando.
“Manifesito ya Tonse Alliance idali yokopa mtima kwabasi n’chifukwa chake anthu adayivotera koma koma zikuoneka kuti adangofunako mavoti chifukwa palibe lonjezo lomwe likuwoneka,” adatero Namiwa.
Wapampando wa mgwirizano wa mabungwe oyima pawokha omwe ali pansi pa National Advocacy Platform (NAP) Benedicto Kondowe adati poyembekezera nthawi yokhazikikayo, Chakwera ndi boma lake akuyenera kufotokoza momwe malonjezowo awakwaniritsire.
“Nzoona kuti malonjezowo ndi ambiri sangakwaniritsidwe nthawi imodzi koma pofika pano akadafotokoza ndondomeko kuti adzakwaniritsa bwanji,” adatero Kondowe.
Kadaulo pa ndale George Phiri adagwirizana ndi Chakwera kuti malonjezo ena sangaoneke mmiyezi 8 yomwe iye wakhala pampando wa upulezidenti.