Nkhani

Ulemu ulibe mkazi kaya mwamuna

Listen to this article

Ulemu ndi khalidwe lofunika pamoyo wa munthu wina aliyense—wamwamuna kapena wamkazi—choncho mtsogoleri wadziko lino sadaphonye kwenikweni masiku apitawa pomwe adakumbutsa amayi za kufunikira kwa ulemu pabanja.

Kungoti langizo labwinoli lidakhala ngati lapotokera mbali imodzi, ya amayi, pomwe abambonso amayenera kuchitako mbali yawo popereka ulemu kwa akazi awo kuti banja liyende bwino.

Kulankhula kotereku kungathe kupititsanso patsogolo maganizidwe aja oika udindo onse oonetsetsa kuti banja lilimbe uli m’dzanja la mayi pomwe bambonso ali ndi mbali yaikulu yoti achite poonetsetsa kuti banja liyende bwino.

Kuphatikiza apo, langizo lakukhala wa ulemu ndi limodzi mwa malangizo omwe amayi akhala akuuzidwa kwa nthawi yaitali, kuphatikizapo ena aja akukhala opirira komanso omvera.

Kotero kuti kufunikira kwa ulemu amayi ambiri akhonza kukhala kuti akukudziwa bwino kuposa abambo chifukwa pachilangizo cha anamwali omwe atha msinkhu kapena omwe akulowa mmbanja, nkhani ya ulemuyi imanenedwa kwambiri.

Amayi enanso ulemuwu saumvetsetsa bwino kotero kuti akamenyedwa salandula konse; mmalo mwake amapepesa bambo owamenyayo, ati ulemu; zomwe zikuchititsa kuti nkhanza za mbanja zisathe.

Choncho mmalo mowirikiza za kufunika kwa ulemu, ndibwino titathandizana kumvetsetsa kuti ulemu ndi chani ndipo kuti uli ndi malire ati makamaka mokhudzana ndi zinthu zomwe siziyenera kuchitika m’banja monga nkhanza.

Kuphatikiza apo, atsogoleri angathandize poika mtima kwambiri pankhani zomwe zikubwenzera m’mbuyo moyo wa amayi ndi mabanja awo. Izi ndi nkhani monga kulephera kwa amayi ambiri kudziimira paokha pa chuma.

Chiwerengero cha amayi omwe akungokhala kudikira kuti athandizidwe ndi abambo chikadali chokwera. Palinso amayi ambiri omwe akukakamira mabanja achizunzo podziwa kuti akalituluka banjalo alibe mtengo ogwira kumbali ya kapezedwe ka chuma. Apa pakufunika kukonza.

Sindikuti amayi azichita mwano m’mabanjamu. Mwano ngosathandiza pabanja ndipo ulemu ndiwofunika zedi. Koma, ulemuwu tiumvetse bwino ndipo uchokere mbali zonse ziwiri—mayi ndi bambo—chifukwa kukhala wa ulemu sikufunika kuti ukhale wa mkazi kapena wamwamuna ndipo aliyense amafuna kupatsidwa ulemu.

Related Articles

Back to top button
Translate »